Ndife wokonzeka kuchititsa zisankho – MEC

Advertisement

Bungwe lowona za zisankho la Malaŵi Electoral Commission (MEC) lanenetsa kuti kuyenda bwino kwa  zisankho zapatatu mu 2025 kudalira kuti anthu amvetse bwino ndondomeko ya kayendetsedwe kazisankhozi.

M’modzi mwa makomishonala a bungweli, Dr Anthony Mukumbwa, anena izi lachinayi ku Mzimba pa msonkhano wolimbikitsa mafumu, atsogoleri a mipingo, mabungwe a Civil Society (CSOs) ndi ena onse okhudzidwa pa nkhani za malamulo atsopano a zisankho komanso ndimomwe malire a madera ndi mawadi anagawidwira.

A Mukumbwa atsindika kufunika kophunzitsa anthu kuti zisankho zichitike bwino pa 16 September chaka chamawa.

Pankumanowu, a Stella Mwachande kuchokera ku bungwe lowona zisankholi adaunikiranso kukonzanso malire a ma ward ndi ma dera a aphungu komwe kumakhazikitsidwa ndi malamulo atsopano kuyambira chaka chatha.

Iwo atiso ngati palibe woyimira pulezidenti wopeza mavoti opitilira 50%, chisankho chakabwereza chiyenera kuchitika mkati mwa masiku 60.

Bungweli la nenetsa kuti tsiku lodzaponya voti pa 16 September, 2025, lidzakhala tsiku la tchuti ndicholinga chakuti anthu ambiri akaponye nawo voti.

Bungweli la bweretsa pamodzi mafumu, azipani, a mabungu, achitetezo komanso atolankhani.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.