Wayamba kukwaniritsa malonjezo Haiya: chithumba cha ligi chakwera

Advertisement
Football Association of Malawi (FAM) President Fleetwood Haiya

…owina tsopano azitenga MK100 miliyoni
…yonse pamodzi yafika pa MK500 miliyoni

Koma apambane ligi chaka chino adya bwino. Yamasula ma bureki TNM, chithumba cha ligi angokhuthula. Malonjezo a Fleetwood Haiya mmbalimo akukwanitsidwa.

Atayamba mokhala ngati akusisitika, kampani ya TNM lero yamwetsa Mkaka anthu okonda masewero mu dziko muno italengeza kuti tsopano yakweza ndalama zimene imapereka ku ligi ya ku Malawi.

Pa mwambo omwe udachitika lero mu mzinda wa Blantyre, kampaniyi yati kuyambira tsopano, ndalama zimene ziziperekedwa ku ligi ya Malawi ndi theka la 1 biliyoni.

Malinga ndi kampaniyi, timu yopambana ligi tsopano izitenga ndalama zokwana MK100 miliyoni kuchoka pa MK40 miliyoni. Pano otenga MK40 miliyoni azikhala nambala 2.

A TNM aonjezeranso kuti iwo tsopano azipereka ndalama yokwana MK3 miliyoni kwa osewera amene azikhala katakwe mu chaka chonse cha mpira.

Kukoma mtima kwa kampani ya foni za m’manja ku kwadza pamene mtsogoleri wa bungwe la mpira wa miyendo mu dziko muno, a Fleetwood Haiya, analonjeza kuti akalowa m’boma azaonetsetsa kuti akweze ndalama zopita ku ligi.

Ndipo a Haiya akamba kuti kukwera kwa ndalama zopita ku ligi ndi umboni oti mfundo zawo zikukwanilitsidwa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.