Magetsi mpwechemphweche ku Tanzania mpaka achita kuthimitsira matchini

Advertisement
Electricity Outage

Pena ngati upemphe kwa a neba kuti mwina angotibwerekako wawo, ife tiwapatse wathu. Chifukwa zimene likuchita dziko la Tanzania ndiye eee ndi zodabwitsa.

Patangopita masiku pa makina a intaneti dzikoli litadya wani ndi sitima za makono, lero dziko la Tanzania lalengeza kuti layamba lathimitsa makina asanu opanga magetsi chifukwa amasowa kopita nawo.

Malinga ndi malipoti ochoka mu dzikolo, ati iwo aona kuti malinga ndi kuchuluka kwa mvula, apanga magetsi ochuluka.

Escom is the supplier of electricity in Malawi
Ku Bagamoyo magetsi akuvutabe

“Tikuchita kusowa nawo chochita magetsi ndiye taona kuti bola tingothimitsa kaye matchini ena,” atero adindo mu dzikolo.

Malinga ndi wailesi youlutsa nkhani ya BBC, aka ndi koyamba kuti dzikoli lichite kufika pogonjetsedwa ndi mphamvu ya magetsi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.