Anthu 331 amwalira pangozi zapansewu m’miyezi isanu

Advertisement

Zotsatira zakafukufuku wa a polisi m’dziko muno zaonetsa kuti anthu 331 ndi omwe amwalira pa ngozi za pa msewu zomwe zachitika mu miyezi isanu chaka chino.

Izi ndimalinga ndi otsatira kwa mkulu ofalitsa nkhani za a polisi m’dziko muno a Thomeck Nyaude.

Anthu ambiri afa pa ngozi chaka chino

A Nyaude ati a polisi ndi omwe anachita kafukufukuyu kuyambira mu mwezi wa Januwale kufikira mu Meyi.

Izi akuti ndi ngozi zochuluka poyerekeza ndi ngozi zomwe zinachitika mu miyezi ngati yomweyi chaka chatha.

A Nyaude anaonjezera kuti gwero la ngozi zoterezi ndi kuyendetsa galimoto munthu ataledzera komanso kunyozera malamulo a pa msewu.

Ngakhale chiwerengerochi ndichokwera kale, pali nkhawa yoti nambalayi ikwera kwambiri potengera kuti apolisiwa sanawerengere ngozi zimene zachitika mwezi wa Juni.

Mwezi watha ndi mwezi umene anthu ambiri m’dziko muno adzaukumbukire chifukwa chakuchuluka kwangozi za pansewu.

M’mweziwu, sipamadutsa masiku osamva zakufa komaso kuvulala kwa anthu pangozi zapansewu zomwe zinapangitsa akuluakulu owona za pansewu kukhwimitsa malamulo a pansewu zomwe sizinaphule kanthu kwenikweni.

Anthu opitilira makumi atatu ndiomwe atisiya pangozi zapansewu mu mwezi wa Juni okha, chiwerengero chomwe ndichokwera kwambiri.

Advertisement

22 Comments

Comments are closed.