Tikhala tikutsimikiza unzika nthawi ya kalembera wa chisakho – NRB

Advertisement

Bungwe la National Registration Bureau (NRB) lanena kuti likhala likutsimikiza unzika, pa nthawi imene bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) likuchita kalembera wa chisankho ndi cholinga choti a Malawi onse apeze mwayi olembetsa nawo mu chisankhochi.

Malinga ndi chikalata chomwe wasayinira ndi Mlembi wamkulu bungweli a Mak Sambo, ogwira ntchito ku bungwe la NRB akapezeka pa centre ili yonse ya MEC kuti athandize nzika zokhazo zomwe zinataya chiphaso cha unzika, nzika zomwe chiphaso chawo chinawonongeka, kufufutika kapena kuthyoka, omwe chiphaso chawo sichikuwerengeka pa makina olembetsela chisankho a MEC komanso omwe analembetsa koma sanakatenge chiphaso chawo cha unzika ku NRB.

“Ogwira ntchito ku bungwe la MEC azikasonyeza anthu ofuna kulembetsa chisankho kuti afike pa malo apadera pomwe bungwe la NRB likakhazikitse pa centre pomwepo, kuti likawathandize asanapitilire ndi ndondomeko yolembetsa mu kaundula wa chisankho cha 2025. 

“Pa malo a NRB, nzika zofunika thandizoli zikalandila umboni wa ka lisiti kosonyeza kuti analembetsa mu kaundula wa unzika. Ka lisiti komwe bungwe la NRB likupereka ndi umboni chabe womwe akagwilitse ntchito polembetsa mu kaundula wa chisankho,” iwo anatero.

A Sambo anapitiliza kunena kuti pa nthawi ya kalembera wa chisankho pa ma centre onse, bungwe la NRB likagwila ntchito yotsimikiza unzika yokha kudzera pa makina a NRB.

Iwo anatsindikanso kuti kwa onse oyenera kulembetsa unzika koyamba, akuyenera kukalembetsa ku ofesi ya NRB.

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lero layamba kalembera wa chisakho Ngati njira imodzi yokozekera chisakho cha 2025.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.