Ubale wanga ndi boma ndi wabwino – Evance Meleka wati sanamangidwe

Advertisement
Evance Meleka

Katswiri pa mayimbidwe a nyimbo, Evance Meleka, watsutsa mphekesera zomwe zimamveka kuti wamangidwa kamba koyimba nyimbo ya “Tasiyana bwanji” pa maliro a mkhalakale pa mayimbidwe Lucius Banda yemweso ndi mwini nyimboyi.

Kumathero a sabatayi pa masamba anchezo panabuka mphekesera kuti apolisi munzinda wa Lilongwe amanga m’modzi mwa akatswiri oyimba, Meleka mokhudzana ndi nyimbo ya malemu Banda yomwe imatchuka ndi kuti “Chigawenga”.

Anthu omwe amafalitsa nkhaniyi amati a Meleka amangidwa chifukwa choimba nyimbo ya “Chigawenga” ku balaka pa maliro a mwini nyimboyi, Banda, ndipo onenawo akuti zimenezi zinakwiyitsa boma mpaka kumukwidzinga woyimbayu.

Koma Lamulungu masana, Meleka wapha mphekesera zonsezi pomwe anazijambura kanema ndi anthu ena angapo, ndipo watsindika kuti mphekesera zoti wamangidwazi ndi bodza la mkunkhuniza.

Mu kanemayi Meleka wati: “Ndi zamabodza, ndili kuno kutumikira Mulungu ku Salima. Anthu ena amasowa zolemba, amasowa zokamba. Ena amangofuna kukuonongera mbiri, ndipo motsimikiza, Evance Meleka ndi boma ubale wathu ndi wabwino kwambiri ndipo ndimalipemphelera dziko la Malawi.”

Gawo lina la nyimbo ya “Tasiyana bwanji” yomwe malemu Banda anayimba ndikutulutsa mu 2002, imati, “Chigawenga mchoipa mtima chimapha munthu, koma ngati boma lichibwezera zasiyana pati.”

Advertisement