‘Tulutsani wanuyo timuone: ngati ali nkhalamba, ife wathu ndi mnyamata’ – wakhazikitsa chipani Nankhumwa

Advertisement
Nankhumwa Malawi

Kuli kanthu mu 2025. Chipani cha People’s Development Party (PDP) chakhazikitsidwa tsopano ndipo a Kondwani Nankhumwa abwela poyera: iwo akutsogolera chipanichi ndipo 2025 akulowa m’boma basi. Inu mufune, kaya musafune.

Poyankhula pa mwambo okhadzikitsa chipanichi omwe wachitikira mu boma la Blantyre, a Nankhumwa ati iwo tsopano athana nazo basi za DPP, tsopano azipanga za PDP.

Pa mwambowu omwe unakometsedwa ndi anthu a molaro omwe amayimba zonyodola anthu ena, a Nankhumwa anafotokoza zambiri zokhudza chipanichi. Mwa zina, a Nankhumwa ati chipani chawo chayima pa nsanamira zitatu.

“Nsanamira zathu ndi zitatu: kulimbikira ntchito, umodzi komanso chakudya chokwanira,” anatero a Nankhumwa uku owatsatira akumenya ng’oma.

Malinga ndi a Nankhumwa, msonkhano wachikulu wa chipani chawo uchitika mwezi wa Agasiti ndipo mipando yonse ya chipanichi izakhala patebulo. Ofuna atha kukatolapo ndithu olo kuchotsa a Nankhumwa kumene ndi kutenga utsogoleri wa chipanichi.

Pamene a Nankhumwa amafotokoza za chipanichi ndiye kuti owatsatira mmbalimu akuyimba ndipo nyimbo imodzi inali yopempha zipani zina kuti zitulutse atsogoleri awo, ati akakhala okalamba, iwo a PDP wawo ndi mnyamata.

Koma a Nankhumwa alengeza kuti chipani chawo sichikufuna kupanga ndale za mtopola kapena zonyozana, ati iwo angofuna kutchaya mfundo zotukula dziko lino.

A Nankhumwa anenanso kuti tsopano chipani chawo sichikuthandizidwa ndi munthu kapena chipani china, maka cha Kongeresi. Anthu akhala akukamba kuti iwo ndi kutheka kuti atumidwa kuti asokoneze chipani cha DPP, koma iwo atsutsa zimenezi.

A Nankhumwa alengezanso kuti kuyambila tsopano, iwo achoka pa Mpando wa mtsogoleri otsutsa mu nyumba ya malamulo. Ati a chipani cha DPP atha kukatenga udindo wawo.

Advertisement