Chakwera alunjika ku USA

Advertisement

Patangopita masiku ochepa chipitireni m’dziko la Kenya, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera akuyembekezera kupita m’dziko la United States of America Lachisano likudzali.

Malingana ndi kalata yomwe unduna owona za ubale wa dziko lino ndi mayiko akunja watulutsa, a Chakwera akuyenera kukakhala nawo pa msonkhano wa zamalonda pakati pa America ndi Africa ku Dallas, Texas, m’dziko la United States of America.

Nsonkhanowu ukuyenera kuyamba pa 6 May, 2024 ndikumaliza  pa 7 May, 2024, ndipo mtsogoleri wa dziko linoyu anyamuka Lachisanu pa 3 May, 2024 kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu International munzinda wa Lilongwe.

Kalatayi ikusonyeza kuti nzika yoyamba ya dziko linoyi, ikupita ku ulendowu mochita kuyitanidwa ndi Boma la US.

Nsonkhanowu upereka mwayi kwa dziko la Malawi kukumana ndi akatakwe osiyanasiyana omwe angathandize chuma cha dziko lino kupita patsogolo, yatero kalayayi.

“Kuwonjezera pa kutenga nawo mbali pa msonkhanowu, wolemekezeka mtsogoleri wa dziko linoyu, akachita zokambirana ndi atsogoleri osiyanasiyana a boma la US komaso akatswiri a za malonda.

“Zokambiranazi zilimbikitsa mgwirizano wa dziko la Malawi ndi dziko la USA pofuna kukwanilitsa masomphenya oti dziko lino likhale lodzidalira lokha pa chuma kudzera mu ndondomeko yogulitsira kunja zinthu zamtengo wapatali mogwirizana ndi masomphenya a Malawi 2063,” yatelo kalatayo.

Undunawu wati a Chakwera akuyembekezeka kunyamuka m’dziko muno Lachisanu nthawi ya 07:40 m’mawa ndipo akuyembekezeka kubwerera kuno ku mudzi Lachisanu, pa 10 May, 2024, nthawi ya 13:35 masana, kudzera pa bwalo la ndege lomweli.

Asanafike kuno ku mudzi, mtsogoleriyu adzayima kaye mumzinda wa Nairobi, m’dziko la Kenya, kumene adzalankhule pa Msonkhano wa Africa Fertilizer and Soil Health (AFSH) pa 9 May 2024, komwe akuti wachitaso kuyitanidwa ndi mtsogoleri wa dziko nzake, William Samoei Ruto.

Advertisement

One Comment

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.