Mudziwitseni Phungu Joseph Nkasa kuti analakwitsa. Mose wa lero ati sanali Mutharika, koma ndi a Timothy Mtambo. Atero eniake pomwe anapangitsa msonkhano wa atolankhani lero pofuna kukumbutsa kuti akadalipo.
A Mtambo amene adachita chete pomwe boma la Tonse lidawapatsa unduna, ndipo samamvekabe ngakhale atachotsedwa, pa 27 April achititsa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe.
Msonkhanowu omwe amachititsa ndi akuluakulu ena a kagulu kawo ka Citizens For Transformation (CFT) cholinga chake chinali choti abwere azawaudze a Malawi kuti akadalipo ndipo iwo apitiriza kumenyera ufulu wa anthu.
Polankhula pa msonkhanowu, a Mtambo adati iwo sazasiya zomenyera ufulu wa anthu chifukwa adasankhidwa ngati Mose wa mu Baibulo kuti adzapulumutse a Malawi.
“Maitanidwe anga ali ngati a Mose, ine ndidasankhidwa kudzapulumutsa a Malawi,” iwo adatero mu chizungu atazunguliridwa ndi anthu ena a ku gulu lawo la CFT.
A Mtambo adaonjezeraponso kuti iwo ali mu boma sikuti anagwirizana ndi zonse zomwe boma limachita. Koma anati sangaulule zomwe sadagwirizane nazo chifukwa adasayinira pangano la chinsinsi.
Mwa zina, a Mtambo adzudzula boma la Chakwera kuti lakanika kusintha zinthu ndipo zina zaonongekeratu.
Iwo adatchula kusowa kwa shuga ndi kwa ziphaso zoyendera ngati zina mwa zinthu zomwe zadzetsa kuwawa m’moyo wa a Malawi.
Koma mmene amayankhula a Mtambo, a Malawi ena pa masamba a mchezo amangowanyodola. Ena ati akuyesa umphawi ndiwo wapangitsa a Mtambo kuti ayambilenso kutakataka.