Kutsatira ulosi omwe nthambi yoona za nyengo mdziko muno inachita ponena kuti mvula iyamba kugwa pa 1 February mwezi uno, tsopano a Malawi ambili ayamikila ulosi wanthambiyi pamene mvula yagwadi m’madera ochuluka ngati momwe nthambiyi inaloselela.
Dzana mneneri wa ku nthambi yoona za nyengo a Yobu Kachiwanda anatsimikizira mtundu wa a Malawi ponena kuti mvula iyamba kugwa mwezi uno pa 1 February pamene pachigawo cha pakati komanso kumwera kwa dziko lino kwakhala kopanda mvula pafupifupi masabata awili.
Kugwa kwa mvula pa 1 February a Salima ndi Kasungu kunafanana ndi zomwe nthambiyi inalosera zomwe zapangitsa a Malawi ambili kutayira ka mtengo nthambiyi.
Pakadali pano alimi okhala mboma la Salima ati ndiwosangalala kamba kamvulayi popeza ng’ambayo ikadatha kuwononga mbewu zawo m’minda pamene zinayamba kuwuma.
Wolemba: Ben Bongololo