Akanganya awili omwe akhala akuchita za umbanda ku Mulanje awanjata

Advertisement
Two theft suspects in mulanje

Apolisi ku Mulanje anjata njonda ziwiri zomwe zakhala zikuzinganiziridwa kuti zakhala zikuchita za umbanda mbomali.

Mneneri wa apolisi ku Mulanje a Innocent Moses watsimikiza za nkhaniyi ndipo iye wati njonda ziwiri mayina awo ndi a Richard Semu azaka 36 zakubadwa komanso a Joseph Elton azaka 32.

Nkhani yonse ikuti apolisi m’bomali anatsinidwa khutu ndi anthu ena pazokhudza njonda ziwiri ponena kuti anthuwo akhala akudabwa ndi makhalidwe anjondazi.

Apa apolisiwo sadazengereze koma kunjata akanganya awiliwa ndipo padakali pano apolisi wa akwanitsa kupeza kanthu osiyanasiyana monga makompyuta, njinga, ma lamya, matiresi, ziwiya zakukhitchini ndi zina.

A Elton ndi a m’mudzi mwa Sikoya mfumu yaikulu Chikumbu ku Mulanje pamene a Semu ndi a m’mudzi wa Nkhumba ku Phalombe ndipo Posachedwapa awiliwa akaonekera ku bwalo lamilandu.

Advertisement