Pamene boma la Malawi limati lilibe ndalama zothandizira aMalawi mazana mazana omwe akhudzidwa ndi ngozi ya madzi osefukira, boma lomwelo laika ndalama yokwana K1.1 biliyoni kuti igwiritsidwe ntchito posamalira maluwa ndi kapinga ku nyumba yachifumu.
Izi zili mu ndondomeko ya za chuma ya chaka chino mpaka chaka chamawa yomwe boma la Malawi lati ligwiritsa ntchito ndalama zokwana K3.78 thililiyoni kusamalira miyoyo ya aMalawi.
Koma fuso mkumati; kodi ndalama yonseyi igwiladi ntchito yosamalira komaso kupindulira aMalawi?
Zadziwika tsopano kuti pa ndalama yokwana K24 biliyoni yomwe nduna ya za chuma Sosten Gwengwe yapeleka kuti igwire ntchito yokozera zinthu zina ku nyumba za chifumu, pali ndalama ina yomwe akuti igwira ntchito yosamalira maluwa, inde kapinga.
Ndondomeko ya zachumayi, ikusonyeza kuti ntchito yosamalira kapinga ndi maluwa ku nyumba yokhala mtsogoleri wadzikoyi, ikufunuka ndalama yokwana K1.1 biliyoni.
Anthu ena mkumadabwa kuti kukoza zinthu ku nyumba za chifumuzi mpaka K24 biliyoni ndipo mwaiyo nkukhala K1.1 biliyoni yosamalilira maluwa ndi kapinga,? Inde ndimomwemo, ndipo a Gwengwe ati izi nzofunika kwambiri.
Sabata ikungothayi iwo awuza nyumba ya malamulo kuti maluwa komaso kapinga zaku nyumba zachifumu sakuyenera kukhala onyentchera komaso ati ku nyumba zachifumuku kuli zinthu zambiri zoti zikozedwe, nchifukwa chake apeleka K24 biliyoni.
“Nyumba ya chifumu ya Sanjika ili ndi vuto la mapaipi omwe akufunikira kuwakonza mwansangansanga. Nyumba ya chifumu ya Kamuzu, ikufunikanso kukonzedwa. Kuli zinthu zina kumeneko zomwe ndi zowonongeka ndipo zikufunika kukonza,” Gwengwe adauza Nyumba ya Malamulo.
Nkhaniyi inabweletsa mpungwepungwe ku nyumba ya malamulo kaamba koti aphungu ochuluka asonyeza kusakhutitsidwa ndi ganizo lopeleka ndalama zonsezi ku ntchito yokoza nyumba za chifumuzi.
Mmodzi mwa a phungu mnyumbayi, yemweso ndi wapampando wa komiti yowona za ndondomeko ya zachuma a Gladys Ganda, ati ndiwodandaula kaamba koti mmbuyomu nyumba za chifumuzi zakhalaso zikulandira ndalama zochuluka.
A Ganda ati mpofunika kuti boma libwera poyera ndi kufotokoza momwe ndalama zomwe zakhala zikupita ku nyumba za chifumuzi zakhala zikugwilitsidwira ntchito.
“Kwa zaka zitatu zapitazi takhala tikupereka ndalama zokwana K5 biliyoni kuti tikonze nyumba zogona mtsogoleri wadziko ndipo lero tikumvaso kuti tikonzenso, kodi nyumba zake ndiziti?
“Kodi nyumba za chifumu zimakonzedwanso chaka chilichonse? Chomwe ndimadziwa nchakuti kukonzanso nyumbazi kumayenera kumachitika pakatha zaka zisanu zilizonse. Kodi tawerengera kale zomwe ndalama za mmbuyomu zagwilira ntchito?” Anafunsa a Ganda.
Phunguyu anadzudzula a Gwengwe popeleka ndalama zonsezi ku nyumba za chifumu ndipo anaonjezera kuti akuluakulu akunyumba za chifumu akuyenera kuwonetsa chitsanzo chabwino pochepetsa ndalama zogwiritsa ntchito.
“Nyumba zaboma ziyenera kukhala zachitsanzo pakuchepetsa mlingo wa ndalama zogwiritsa ntchito; apo ayi ndikuona kuti iyi ndi ndondomeko ya zachuma yomwe itha kugwiritsidwa ntchito molakwika kwambiri,” anaonjezera Ganda.
Nkhaniyi yakwiyitsaso aMalawi ochuluka maka mmasamba a nchezo omwe ati ndi kwabwino ndalama zokozera maluwazi zinakagwiritsidwa ntchito yothandizira anthu omwe akhudzidwa ndi namondwe wa Freddy.
“K1 biliyoni imeneyo ikanatha kugwira ntchito pomanga nyumba 588 za anthu omwe akhudzidwa ndi namondwe monga yomwe wamangitsa Kondwani Kachamba, koma tsokalo boma laganiza zogwiritsa ntchito kutchetchela ndi kudzalira maluwa ku nyumba ya pulezidenti kwinako zikulowa mmatumba mwa anthu. Timachita nthabwala kwambiri ngati dziko,” munthu wina wadandaula pa tsamba la nchezo.
Zosezi zikubwera pomwe boma lapeleka K1.6 biliyoni yokha kuti ithandizire anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi kaamba ka namodwe wa Freddy yemwe wapangitsa kuti anthu pafupifupi 700 sausande akhudzidwe.
Ndipo m’mawu ake mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anati boma palokha lilibe ndalama zoti nkuthandizira anthu okhudzidwawa ndipo linapempha anthu, ma kampani ndi ma bungwe kuti agwirane manja pothandiza anthu okhudzidwawa.
Follow us on Twitter: