Mutharika asambwadza Chakwera

Advertisement

…ati anthu akudzipha kwambiri kaamba koti alibe chiyembekezo
…ati MCP ikufuna kudzabela chisankho 2025

Mtsogoleri wakale wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Peter Mutharika, asambwadza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ponena kuti mavuto onse omwe ali mdziko muno ndi kaamba koti a Chakwera alephera kulamulira.

A Mutharika amayankhula izi lachisanu pa 11 November kunyumba yawo ya Page m’boma la Mangochi komwe anachititsa msonkhano wa olemba nkhani komwe awuza a Chakwera kuti atule pansi udindo poti alephera kuyendetsa bwino dziko lino.

Iwo ati mavuto monga kusowa kwa mafuta, kusowa kwa ndalama za kunja, kuthimathima kwa magetsi, kukwera mitengo kwa zinthu ngati chimanga komanso fetereza, ndichitsimikizo choti a Chakwera alepheleratu kuyendetsa dzikoli.

A Mutharika adzudzulanso a Chakwera pokonda kuyenda maulendo akunja komaso mdziko muno zomwe ati zikukolezera mavuto adzaoneni omwe ali mdziko muno kaamba koti mmaulendo ngati amenewo ndalama zankhaninkhani za misonkho ya a Malawi zimasakazidwa.

Apa mtsogoleri opumayo anati boma la a Chakwera litengele zomwe iwo amachita nthawi ya ulamuliro yawo ponena kuti iwo samayenda kwambiri. Malingana ndi a Mutharika, a Chakwera ayenda ma ulendo akunja 34 mu zaka ziwiri zokha.

“A Chakwera atule pansi udindo ndipo pakhale boma longoyembekezera kuti likonze zinthu komanso lichititse zisankho zina za mtsogoleri wa dziko.

“Tangoganizani mumzaka ziwiri zomwe walamulirazi, wayenda kale maulendo oposera 34. Ngakhale kuti sindikukumbuka kuti ndinayenda mochuluka bwanji, koma muulamuliro wanga maulendowa sanafike mpaka 34.

“M’malo mochepetsa maulendowa nthawi ngati ino yomwe dziko lino lili pa mavuto, iye mpamene akutenga anthu 250 kupita nawo kunja kokajambulitsa zithunzi. Sakusamalaso za mavuto omwe anthu akukumana nawo mdziko muno,” atelo a Mutharika.

A Mutharika adzudzulaso boma la a Chakwera kaamba kakukula kwa mchitidwe wa katangale zomwe akuti zapangitsa kuti ndalama zakunja zisowe mdziko koma ati iwo momwe amatuluka m’boma anasiya ndalama zakunja zochulukwa kwambiri kupitilira

Kupitilira apo, a Mutharika ati mdziko muno mchitidwe odzipha wachuluka kwambiri pano ndipo ati izi ndi kaamba koti anthu ochuluka ataya chiyembekezo chomwe anali nacho ndi boma la Tonse motsogozedwa ndi a Chakwera.

“Masiku apitawa ndimacheza ndi katswiri wina owona za matenda a maganizo. Mu kuyankhula kwake iyeyo anadabwa kuti mchifukwa chani m’dziko muno anthu akudzipha kwambiri. Ine ndili ndi yankho, anthu akudzipha chifukwa ataya chiyembekezo ndi boma ili,” ateloso a Mutharika.

Iwo anati ndiodabwa kuti vuto la kusowa kwamafuta agalimoto lafika posauzana chonchi pamene iwo momwe amachoka m’boma adasiya ku nkhokwe za mafuta kuli mafuta a galimoto okwanira masiku ochuluka kwambiri, pafupifupi 160.

Mtsogoleri wa chipani cha DPP yu wauluraso kuti chipani cha MCP chayamba kupanga upo ofuna kudzabera chisankho cha mchaka cha 2025 ndipo ati mwazina chipanichi chalemba ntchito mmodzi mwa mamembala ake a Andrew Mpesi ngati ogwira ntchito ku bungwe loyendetsa chisankho la MEC zomwe ati ndi zosaloledwa ndipo ati mkuluyu achotsedwe paudindowu.

“Kongelesi ili ndi lingaliro lodzabera chisankho cha 2025 ndipo Ife izi tazitulukira. Panopa alemba ntchito mkulu wa bungwe la MEC (chief executive officer) yemwe m’ngwa Kongelesi. Panopa tamvanso kuti kwayambika kalembera wa unzika wa tiana komanso olo panopa kuti munthu ukonzetse chiphaso cha unzika chikatha mphamvu zikumakhala zovuta ukakhala kuti umachokera madela omwe Kongelesi siyotchuka. Zonsezi akuzembera kudzabera chisankho,” anaonjezera motelo a Mutharika.

A Mutharika apempha bungwe lothana ndi ziphuphu la ACB komanso nthambi ya polisi yoona milandu ya ndalama kuti ikhazikitse kafukufuku pa zakusakazika kwa ndalama zokhudza zipangizo za ulimi zotsika mtengo za ndondomeko ya AIP.

Iwo ati ndizokhumudwitsa kuti madera ena mdziko muno ayamba kulandira mvula, ngakhale alimi sanayambe kupeza zipangizo za ulimi ndipo awuza boma la a Chakwera kuti liwonetsetse kuti pakutha pamwezi uno feteleza otsika mtengo ayambe kupezeka m’madera onse.

Advertisement