Mtsogoleri wakale wadziko lino a Peter Mutharika ati mchimwene wawo malemu Bingu Wa Mutharika anachita kuphedwa pothililidwa poyizoni mu chakumwa chawo ndipo ati amawadziwa anthu omwe anachita izi.
A Mutharika amayankhula izi la mulungu ku nyumba yawo ya Page ku Mangochi komwe iwo pamodzi ndi akuluakulu ena achipani cha DPP anachititsa nsonkhano wa atolankhani komwe amakamba zinthu zosiyanasiyana.
Mtsogoleri wakaleyu anati malemu Bingu sanamwalire imfa yachilengedwe ndipo ati anthu omwe sanawatchule ndi omwe anachita chipongwechi pomuthilira poyizoni mu chakumwa chake chomwe anamwa patsikuli.
A Mutharika ati cha m’ma 8 koloko m’mawa wa tsiku lomwe a Bingu anamwalira, munthu wina anatenga poyizoni ndikuthira mu chakumwa cha malemuwa ndipo cha m’ma 10 koloko m’mawa omwewo, a Bingu anamwalira.
“Ndizoona kuti Bingu anathililidwa poyizoni mumchakumwa chake. Poyizoni anaikidwa mujuwisi wawo chamma 8 koloko mmawa ndipo mmene imati 10 koloko mmawa omwewo , a Bingu anamwalira ndi nthenda yokhudza mtima.
“Panalibe vuto lililonse ndi mtima wawo kapena chili chonse chokhudza zimenezo. Ndizoona ndithu ndipo ndimawadziwa anthu omwe anapanga izi. Anali mchimwene wanga ndipo sindinganame pankhani ngati iyi,” atelo a Mutharika.
Mtsogoleri opumayi yemweso ndi mtsogoleri wa chipani cha DPP wati iwo ndi akubanja anaganiza zongoyisiya nkhaniyi ponena kuti amaona kuti kuyamba milandu yankhaniyi sizinali zoyenera kwa iwo komaso kwa dziko la Malawi.
Malemu Bingu omwe anabadwa pa 24 February mchaka cha 1934, anamwalira pa 5 April mchaka cha 2012 pomwe anali ku nyumba yachifumu ya Kamuzu mumzinda wa Lilongwe ndipo anaikidwa pa 23 April ku Mpumulo wa bata ku malo awo Ndata m’boma la Thyolo komwe iwo amachokera.
Thanks for the information about our former president bingu wa mthalika if he was still alive maybe we could’ve seen the change to better not like this time.