Zija amayankhula wachiwili kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima zoti anagwilizana ndi a Lazarus Chakwera kulandilana mu 2025 ati ndi zamkutu komanso zongopeka. A Kongeresi alibe mgwilizano umenewo.
Malingana ndi mlembi wamkulu wa chipani cha Kongeresi, a Eisenhower Mkaka, chipani cha MCP chilibe ma pepala a mgwilizano amene akukamba a Chilima.
Iwo anena izi pa msonkhano wa atolankhani omwe anachititsa ku likulu la chipanichi ku Lilongwe pofuna kuthililapo ndemanga pa zimene a Chilima anaudza dziko la chisanu madzulo.
Malingana ndi a Mkaka, chipani cha MCP chilibe buku la mgwilizano limene a Chilima amawelenga.
A Chilima pachisanu anadzudzula mkhalakale za MCP ati kamba kodzetsa mpungwepungwe mu mgwilizano wawo pomati a Chakwera ayimanso 2025.
Follow us on Twitter: