Nduna yoona zamphavu yamagetsi a Ibrahim Matola awuza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti asamvele achule omwe akufuna kuti a Chakwera asiye kuyendayenda, ndipo a Matola ati dziko lino likuyenda bwino.
A Matola amayankhula izi Lolemba pa 6 June ku Golomoti m’boma la Dedza komwe mtsogoleri wa dziko linoyu amakhazikitsa ntchito yapanga mphamvu yamagetsi kuchokera kudzuwa.
Ndunayi inati anthu ambali yotsutsa boma akusocheletsa anthu mdziko muno pomanena kuti zinthu sizili bwino ndipo inadzudzula akuluakulu achipani cha DPP kaamba kowuza a Chakwera kuti achepetse maulendo akunja komaso mdziko mom’muno.
“Posachedwaoa apulezidenti mukhala mukuyenda, ndiposo tisawamvele achulewa amene akunena kuti osamayenda, osamayenda. Tikufuna kuti adziwe kuti inuyo mudalonjeza ndiposo zikuchitika,” watelo Matola.
Ndunayi yatsutsa mwantu wagalu kuti zinthu sizikuyenda mdziko muno ndipo wati kukhazikitsidwa kwa ntchito yamphamvu yamagetsi kuchokera kudzuwa ndichitsimikizo chakuti makampani ambiri akunja ali ndi chidwi chothandiza dziko lino.
Apa a Matola anaonjezera kuti zinakakhala kuti mayiko komaso mabungwe sakugwilizana ndi ulamuliro wa Tonse, sibwezi atabwera ku Malawi kuno kudzachita zitukuko zomwe ndikuphatikizapo kukhazikitsidwa kwa malo opangira magetsiwa.
Iwo analamula a Chakwera kuti ajambulitse chithunzi ndi akazembe amaiko akunja komaso oyimilira mabugwe osiyanasiyana omwe anapezeka pamwambowu ngati umboni kuti dziko lino lili paubale wabwino ndi maiko ena komaso mabungwe akunja.
“Chithuzichi, ndimafuna ndipeleke umboni chifukwa matchona ena ake sabata yapitayi adakungana nkumauza atolankhani kuti dziko la Malawi latha. Ukamawerenga nyuzipepa, ukumangoti basi tikamadzuka mawa tipeza dziko la Malawi kulibe.
“Nde anthu ajambulidwa apawa angabwere ku Malawi kudzapeleka chuma chawo ku dziko lakutha? Maiko akunjawa sanangobwela ku Malawi kuno iyayi, koma atsata upangiri ndi utsogoleri wa a Chakwera,” anaonjezera chonchi Matola.
Ndunayi inalamulanso ma kampani omwe anasainirana mgwirizano ndi boma pankhani yopanga magetsi, kuti ngati sakhala atayamba kugwira ntchito yomwe anagwirizana pa masabata atatu akudzawa, boma kudzera ku unduna wawo lithetsa migwirizanoyo.
Follow us on Twitter: