Limodzi mwa mabungwe omenyera ufulu mdziko muno la Center for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) lati a Ken Kandodo omwe anali nduna ya za ntchito akuyenera amangidwe pankhani yakusakazidwa kwa ndalama za mlili wa covid-19.
Nkhaniyi ikubwera pomwe lamulungu lapitali mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera achotsa paunduna a Kandodo powaganizira kuti alimugulu la anthu omwe asazakaza ndalama zokwana K6.2 billion zomwe zimayenera kugwira ntchito yolimbana ndi mlili wa Covid-19.
Malipoti akusonyeza kuti a Kandodo anagwiritsa ntchito ngati ma alawasi ndalama zokwana K614, 000 zamuthumba la covid-19 pomwe iwo anawapelekeza a Chakwera kupita ku South Africa kumapeto kwa chaka.
Ngakhale zili choncho a Kandodo akukana kuti iwo sanazakaze ndalamazi ponena kuti iwo pomwe amalandira ndalamazi sanauzidwe kuti zikuchokera muthumba lolimbana ndi mlili wa covid-19 ndipo ati yemwe akudziwa komwe ndalamazi zinachoka ndi mlembi wa mkulu ku undunawu.
“Maunduna onse aboma mmene zimakhalira mmonena kuti amene amapanga zonse zokhudza ndalama ndi a Principal Secretary ndi anthu ena, koma kukakhala kuti kuundunawo kuli wachiwiri kwanduna, anthu awiriwa siziwakhudza amangolandira zomwe mlembi wamkulu wakoza.
“Nkhani yomwe ikunenedwayi ndinkhani yokhudza ma alawasi omwe ine ndinalandira pomwe timapita kunja kwa dziko lino mu November chaka chatha. Zonse zokhudza ulendowu anapanga ndi mlembi wamkulu, ineyo ndinangolandira, sindimadziwa kuti zachokera akaunti iti,” atelo a Kandodo.
A Kandodo anapatsidwa ndalama za Covid-19 zokwana K614, 000 mu Novembala chaka chatha ngati ma alawasi paulendo owapelekeza a Chakwera ku South Africa. Ndalamazi zinabwezedwa mu February chaka chino.
Izi zabweretsa mafunso ochuluka pakati pa anthu ambiri ndipo ena akuti ichi ndichitsimikizo kuti a Kandodo akuvomereza kulakwa kwawo pankhaniyi.
Malingana ndi mkulu wa bungwe la CHRR a Michael Kaiyatsa, zomwe achita a Kadondo pobweza ndalamazi, ndiumboni waukulu woti iwo akuvomera kuti anasakazadi ndalama zikunenedwazi.
Apa a Kaiyatsa ati chomwe chikufunika pano mchoti apolisi asachedwechedwe koma amange a Kandodo ndipo ati ngati angapezeke olakwa akuyenera kulandira chilango molingana ndi malamulo adziko lino.
Pakadali pano apolisi sanamangebe a Kandodo koma mneneri wa apolisi mdziko muno a James Kadadzera ati onse omwe akukhudzidwa ndikusakazidwa kwa ndalamazi, amangidwa ndipo lamulo ligwira ntchito.
Chiwerengero cha anthu omwe amangidwa mokhudzana ndikusakazidwa kwa ndalamazi chakwera ndipo chili pa 31 tsopano potsatira kumangidwaso kwa anthu ena khumi ndi awiri lolemba.