Musamangokuwa za mafuta muzifunsa kuti m’chifukwa chani – Usi

Advertisement
Usi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Michael Usi awuza anthu amene anasonkhana pa nsika wa Lunzu m’boma la Blantyre kuti asamangokuwa za kusowa kwa mafuta koma adzifunsa kuti zina zikuchitika chifukwa chani ndi pamene adzakhale anzeru.

A Usi omwe analowa mu msika wa Lunzu kugula zinthu monga, Gaga, tomato, utaka, ziwala ndi zina, atatuluka mu m’sikamu anawuza anthu kuti m’boma mumakhala zinthu zambiri ndipo si zonse zomwe boma likuyenera kuwuza anthu ponena Kuti kutelo ndekuti zinthu zina siziyenda.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wadzikoyu wapeleka chiyembekezo kuti zinthu zikhala bwino pamene anati anthu ambiri sakudziwa m’mene zinthu zimayendera m’boma ndipo kwawo m’kungokuwa zili patali.

“Pena anthu muzifunsa mafunso kuti kodi mafuta akusowa chifukwa chani? Kenako muzikambirana nde mudzakhala a nzeru,” anatelo a Usi.

Mu ulendo wawo ochokera ku Lilongwe lero lachinayi kupita ku Blantyre komwe ati akhaleko sabata ya thunthu, iwo ati ayenda m’midzi kuthandiza anthu kulima komanso kuwapatsa feteleza ndi mbewu za ulele zomwe apempha kwa akufuna kwabwino.

Iwo anawonjezera kunena kuti kukhala ndi udindo kapena ayi ndi zinthu zopanda phindu ngati sizikupindulira anthu, iwo anawonjezera kuti patsogolo pa zonse pakhale kuyang’ana mavuto a anthu.

Advertisement