Alamulidwa kukhala ku ndede zaka 53 kamba kopha amuna awo

Advertisement
Mumba

Oweluza milandu Mzondi Mvula walamula a Annie Mumba kukakhala kundende kwa zaka 53 pa mlandu omwe bwalo lawapeza olakwa pakupha amuna awo malemu Prof. Peter Mumba.

Powelenga chigamulo chake, Mvula anati zomwe anapanga mayiwa omwe pano ali ndi zaka 56, ndizodabwitsa kamba koti anadikila ambulance kuchokela ku Bunda mtunda wa 20km pamene akanatha kupita nawo amuna awo kuchipatala chomwe ndi mtunda wa ma kilomita asanu pomwe amamva kupweteka m’mimba.

Mvula anati bwaloli kutengela ndi umboni womwe unabwela anapeza kuti imfa ya Mumba inali yokayikitsa (yochita kukonza).

Malemu Mumba anaphedwa ndi mkazi wawo (Annie) zaka zinayi zapitazo atadyetsedwa chakudya chomwe munali chiphe kunyumba kwawo.

Iwo anali mphunzitsi wa phunziro la Chemistry pasukulu yaukachenjede ya LUANAR.

Advertisement