
Zatsogolo lotuluka pa belo kwa Tumpe Mtaya ‘Phwedo’ zidziwika mawa Lachisanu pomwe Chief Resident Magistrate Benjamin Chulu wati adzaweluza pa pempho la belo 2 koloko masana.
Oyimila mbali ya boma pa mlanduwu anapempha oweluza mlandu kuti alore kuti Phwedo akhalebe omangidwa ndipo adzimusungabe kwa masiku asanu kuti amalizitse kafukufuku wawo.
Koma oyimila ozengedwa anati mbali ya boma yakanika kupeleka mfundo zolula (zokhwima) zomwe zingapangitse kuti ochita zisudzoyu akhale akumusungabe m’chitolokosi kudikira kutha kwa kafukufuku.
Loya wina wa Phwedo, Stain Chirwa anati nzodabwitsa kumva kuti oganizilidwayu akasokoneza umboni chifukwa ndi odziwika pamene sakudziwa nkomwe mboni zomwe aboma agwiritse ntchito.
Chirwa anati kukhala otchuka sikungalepheretse oganizilidwa kutuluka pa belo pomwe anayelekeza chitsanzo cha milandu ya akulu akulu ena otchuka aboma monga mlandu wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko yemwe anatulukanso pa belo koma ati sanadasokoneze umboni n’komwe.
Katswiri wa mu Kanema wa ‘School days’ yu anamumanga Lachiwiri, ndipo lero amuwelengela milandu yake iwiri, oyamba ndiwo oganizilidwa kuti anasosola nthenga za mwana osakwana zaka za m’malamulo (18) ndi wina oganizilidwa kuzembetsa mwana