A Chakwera ayamikira atsogoleri a mpingo wa katolika ndi mayiko awo pogwira dzanja Malawi

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwera wayamikira mpingo wa katolika motsogozedwa ndi ma Bishop ake maka mayiko a Zimbabwe ndi Zambia ponena kuti mayikowa agwira dziko la Malawi pa mkono mnyengo za mavuto.

A Chakwera anayankhula izi pa mwambo otsekulira msonkhano wa atsogoleri a mpingo wa katolika a mayiko atatu a Zimbabwe, Malawi ndi Zambia omwe uchitikire kuno ku Malawi m’boma la Salima.

A Chakwera ati dziko la Malawi lawonetseledwa Chikondi chambiri ndi mayiko olizungulira kuyambira pamene Malawi amadutsa mu nyengo ya matenda a Covid 19, mphepo zowononga monga Cyclose Anna ndi Gombe, matenda a kolera omwe anatenga miyoyo, mvula yosakaza yodza ndi mphepo yotchedwa cyclone Freddy chaka chatha komanso pamene dziko la Malawi linataya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko a Saulos Chilima ndi ena 8 pa ngozi ya ndege mwezi wa June.

“From the bottom of my heart thank you for your solidarity and thank you for your prayers and I wish you a great conference” [kuchoka pansi pa mtima wanga zikomo kwambiri chifukwa chotigwira dzanja mthawi ya mavuto, zikomo chifukwa cha mapemphero anu, ndukufunirani mkumano wabwino”] anatero a Chakwera.

Mtsogoleri wa dzikoyu wati mkumano wa atsogoleri a mpingowu ndi ofunika ndipo ukhala mu mbiri ya dziko ponena kuti ndi zokondweletsa kuti Malawi ndi dziko limene lichititse mkumanowu koyamba.

Msonkhano wa ma Episikope oposa 20 a mpingo wa katolikawu uyamba mawa lachitatu kufikira lachinayi pamene adzawuze anthu zomwe akambirana mu mkumanowo kudzera kwa atolankhani.

Advertisement