Inkosi Kwataine ya m’boma la Ntcheu yadandaula kuti anthu opeleka chiyembekezo ochokera m’bomali amafa mosadziwika bwino ndipo ati ndiodabwa kuti anthu akuuzidwa kuti asunge bata pamene imfa ya yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Saulos Klaus Chilima ndiyosamvetseseka.
Inkosi Kwataine imayankhula izi Loweluka pa malo okwelera bus m’bomali pomwe panachitikira mwambo oyatsa makandulo pokumbukira yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Chilima omwe anafa pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu pangozi ya ndege.
Iwo ati ndiodabwa kuti anthu angapo omwe ankapeleka chiyembekezo kwa anthu m’bomali pa ndale, anafa mosadziwika bwino, ndipo mfumuyi inapelekera chitsanzo cha imfa za malemu Dick Matenje, malemu Albert Andrew Muwalo, malemu Sam Mpasu zomwe akuti zinali zosamvetsetseka.
Mfumuyi yomwe inafika popukusa mutu kuli kusamvetsetsa, yaulura kuti a Chilima atamwalira m’maofesi mwa mafumu m’bomali mwakhala mukupita adindo ena kumawauza mafumuwo kuti alangize anthu awo kuti asunge bata pa nthawi yangoziyi.
Inkosi Kwataine yati, “Sindikulira Saulos Chilima yekha ayi, ndikulira kuyambira a Matenje, Sam Mpasu ndi angoni onse aku Ntcheu kuno amene tinkaloza kuti awawa tsiku lina awa (adzatithandiza), komatu zimangothera momwemo.
“Pano tikuuzidwa kuti chitani bata; nthawi yomwe ankamwalira a Matenje ndikuwadziwanso omwe ankatiuza kuti chitani bata. Kodi batali tipanga mpaka liti? Ife tikukhala ndi bata koma ana athu akungopita nde batali tikhala nalo bwanji?”
Mfumuyi yatinso zimakhala zodabwitsa kuti maliro a anthu akuluakulu ochokera m’bomali pamakhala asilikali onyamura mfuti ochuluka monga momwenso zinalili pa maliro a malemu Chilima ku Nsipe m’boma la Ntcheu.
Iwo awonjezera kuti pano ali ndi mantha kwambiri chifukwa sakudziwa kuti munthu winanso ndindani amene angaloze kuti ndi chiyembekezo cha anthu a mtundu wa chingoni.
Inkosi Kwataine yafotokoza malemu Chilima ngati munthu yemwe ananyamula chiyembekezo cha anthu ochuluka kwambiri m’dziko muno, komanso ati anali nsanamira ya anthu a mtundu wa chingoni.
Malemu Chilima pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu, anamwalira pa 10 June 2024 potsatira ngozi ya ndege yomwe anakwera patsikuli pomwe ankapita ku mwambo wa maliro wa malemu Ralph Kasambara.