‘Thandizani osowa’ – Asilamu apemphedwa pa nyengo yokondwelera Eid Al Adha 

Advertisement
Eid Al Adha

Asilamu m’dziko muno awapempha kuti akhale othandiza osowa pomwe akusangala tsiku la Eid Al Adha lomwe amapha ziweto monga mbuzi, ng’ombe ndi nkhosa ndikupereka kwa anthu omwe ali osowa.

M’modzi mwa akulu akulu a Bungwe la Bena Charity Trust lomwe ndi la chipembedzo cha chisilamu a Precious Kasopa ndiwomwe ayankhula izi ku Zomba pomwe bungwe’li limagawa nyama ya mbuzi kwa anthu osiyana siyana posatengera chipembedzo kapena mtundu.

A Kasopa ati chipembedzo cha chisilamu chimagawa nyama kwa anthu potengera momwe Mulungu adamuuza Abraham/Ibrahim kuti apereke nsembe mwana wake Ishmael choncho kumakhala kupereka nsembe ngati kugonjera lamulo la Mulungu.

Iwe adati nyengo ya Eid Al Adha imabweretsa umodzi chifukwa anthu amakhala pamodzi kupanga chisangalaro chogawana nyama komanso kuthandiza osowa.

Pamenepa a Kasopa afunira asilamu onse m’dziko muno kuti asangalale mwatendere panthawi ino komanso adapempha asilamu onse kuti apemphelere mizimu ya anthu asanu ndi anai kuphatikizapo yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Saulosi Klaus Chilima omwe adamwalira pangozi ya ndege munkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba Lolemba sabata yatha ndipo alowa m’manda lero ku mudzi kwawo ku Nsipe m’boma la Ntcheu.

“Ife a Bungwe la Bena Charity Trust lomwe ndilachipembezo cha chisilamu tidaganiza zokupha mbuzi kuti tigawire abale athu omwe ali osowa komanso kuti tikhale pamodzi ndikusangala limodzi pamwambo wa Eid Al Adha,” iwo datero.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.