Nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ati akubanja komanso abale a wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima apempha kuti pa mwambo wa maliro pasakhale ndale zilizonse potengera kuti eni akenso sakanakondwa kuti zitero.
Poyankhura pa msonkhano wa atolankhani lero, a Kunkuyu ati akudziwa kuti anthu ambiri akonza zinthu zosokoneza pa mwambo wa maliro wa malemuwa koma akubanja apempha kuti zisatero.
Iwo adawonjezera ponena kuti nkhani zambiri zomwe a komiti ya maliro akumva kuchokera kwa abale komanso akubanja a malemuwa nzopempha kuti maliro ayendebwino chifukwa zoyankhura za mwini wake zinali zoti mwambo wake wa maliro udzayende bwino.
“Taona kale pa masamba a mchezo pakuyenda pologalamu ya maliro a mayi Patricia Shanil Dzimbiri, zomwe zikusonyeza kuti eni ake amaona kuti tsiku lawo lochoka pa dziko lino layandikira ndipo mzimu wawo umawayankhura”, adatero pototokoza.
Ndunayi yachenjeza anthu omwe akhala akutumiza zithunzi zokhunza ngoziyi kuti asiye kamba koti zitha kubweretsa chisokonezo chifukwa choti nkhaniyi ili mkati mofufuzidwa.
A Kunkuyu ati thupi la malemuwa alitengera ku nyumba ya malamulo Loweruka komwe likagone ndipo mwambo wake atsogolere ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.
Masanawa, kunali mwambo wa misa ku mpingo omwe malemuwa amapemphera ku area 18 ndipo utatha mwambowo, thupili analitengera ku nyumba yawo ya boma ku area 12 komwe ligone mpaka Loweruka.
Mwambo waukulu uchitika Lamulungu pa bwalo la zamasewero la Bingu.
A Chilima komanso a Shanil Dzimbiri ndi Chisomo Chimaneni (Ntchisi), Dan Kanyemba (Lilongwe), Colonel Owen Sambalopa (Zomba), Major Wales Aidin (Mangochi), Flora Selemani Ngwirinji (Thyolo) and Lukas Kapheni (Kasungu), amwalira pa ngozi ya ndege yomwe inachitika lolemba mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.