Nzika yaku Nigeria yagwidwa ndi cocaine 

Advertisement
Paul Chizetere Osuaha

Apolisi m’boma wa Lilongwe amanga nzika ya m’dziko la Nigeria yazaka 43 kamba kopezeka ndi timaphukusi 33 ta mankhwala ozunguza ubongo a cocaine. 

Malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa za polisi mchigawo cha kumadzulo mchigawo chapakati a Foster Benjamin, oganizilidwawa azindikilidwa ngati Paul Chizetere Osuaha.  

A Benjamin ati Osuaha amangidwa usiku wa Lachisanu pa 24 May 2024 pa malo ena omwera chakumwa chaukali otchedwa Pamowa ku Area 49 New Gulliver m’boma la Lilongwe. 

Wofalitsa nkhaniyu wati a Osuaha anapita ku malowa kukagulitsa mankhwala oletsedwawa ndipo ali nkati mogulitsa, munthu wina anakatsina khutu apolisi omwe sanachedwe koma kumuthira unyolo mkuluyu. 

Potsatira izi apolisiwa anapita ku nyumba kwa oganizilidwayu kuti akachite chipikisheni komwenso anakapeza timaphukusi tina ta mankhwala ozunguza ubongowa komanso ndalama yokwana K1 miliyoni. 

Paul Chizetere Osuaha akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu wopezeka ndi mankhwala owopsa popanda chilolezo.

Advertisement