Neba mutu sukugwila: Mzuzu City Hammers 2, Wandalazi 0

Advertisement
Mzuzu City Hammers

Awa za ligi sizikuwakhudza. Za mpira ndi kutheka si mbali yawo. Chifukwa atagogodedwa sabata latha, leronso akhomedwa. Manoma ayenda wabule ku Mzuzu. Azibwelera chotsimphina. Mmalo motamangitsa matimu, iwo ndi amene akutamanga. 

Pa masewera amene akondoweza mzinda wa Mzuzu, timu ya Mzuzu City Hammers lero yaphunzitsa phunziro anyamata a Mighty Wanderers. Mavuto a nyerere anayamba chigawo choyamba pamene anyamata a Hammers anaonetsetsa kuti alendo awo asapume.

Khama la Hammers linapindula patadutsa mphindi 15 pamene mnyamata wawo Isaac Msiska anasumbila mpira mu ukonde kuti amwetse wa mkaka onse owatsatila ndi wa ganyu. Anaoneka kututumuka anyamata a nyerere kuyesera umu ndi umu kuti azionjole koma sanadziwe mtima wa Msiska.

Pamene oyimbila anaonjezera mphindi ziwiri kuti mwina nyerere zibwenze asananyamukeko wokakalipidwa ndi a Ramadan, Msiska anakodoleramo chigoli china kuti anyamata a Wanderers apite kopuma atalasidwa bwino ndi jekeseni waukali.

M’mene amapita kukapuma ndiye kuti nyerere zitachita chidima, zikhomo zomwe anaona ku Lilongwe m’manja mwa ma Banker zikuoneka kuti zikupitilira.

Mu chigawo chachiwiri, timu ya Noma inayetsetsa koma anyamata a Mzuzu City Hammers sanalole zachibwana. Kwinaku masapota awo akuimba za chipongwe kunyodola anyamata a Noma amene anathamangitsidwa bwino lomwe.

Potha pa mpira, Mzuzu City Hammers 2 pamene alendo awo a Noma chimanjamanja basi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.