Mitengo ya shuga yovomerezeka yakwera, ngakhale sakupezeka

Advertisement
With the cost of living on the rise, prices of Sugar in Malawi have also peaked in recent years to the extent that very few can afford the product.

Kampani yopanga Shuga ya Illovo yalengeza kuti tsopano yakweza mitengo ya shuga wake amene sakupezeka molongosoka pa msika.

Mu chikalata chimene kampaniyi yatulutsa, iyo yati kuyambira lolemba pa 22 April, ikhala ikukweza mitengo ya shuga. Tsopano paketi la 1kg akuti mtengo wake ovomerezeka ndi MK2300. Mtengowu achotsa pa MK1700.

Ngakhale kuti kampaniyi yalengeza zakukwera mtengo kwa shuga, ndi kovuta kuti anthu ambiri amupeze pamsika. Kuyambira ku mapeto kwa chaka chatha, anthu akhala akusaukira kuti apeze shugayu pamene zidamveka kuti wagulitsidwa ku mayiko ena ngati Zimbabwe.

Kusowa kwa shuga kunapangitsa kuti ma wokala a mu makwalala ambiri azimugulitsa pakati pa mtengo wa MK3500 ndi MK5000. Sizikudziwika kuti ndi kukweza kwa mtengo ovemerezekaku kupangitsa kuti afike pa ndalama zingati mu ma wokala a mu makwalala.

Anthu ena aonetsa chiyembekezo ndi kukweraku, kuyesa kuti mwina tsopano shuga ayamba kupezeka ochuluka pamsika.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.