Palibe kothawira, nayo kampani ya Salima Sugar yakweza mtengo wa shuga wake

Advertisement
Salima Sugar

Kokapumira ndi kumwamba basi. Patangotha ma ola bungwe la Blantyre Water Board litalengeza kuti lakweza madzi ndinso kampani ya Illovo italengeza kuti shuga wake yakweza, nayo kampani ya Salima Sugar yalowa m’bwalo pofuna kuonetsetsa kuti anthu asamwenso thiyi basi. Akweza sugar wawo.

Malinga ndi kampaniyi, iwo ati shuga wawo amene amagulitsa pa mtengo wa MK1900 tsopano naye wakwera ndi MK300 monga yachitira kampani ya Illovo. Shugayu wafika pa MK2200.

Izi zikudza pamene mu dziko muno Shugayu adakali osowa kwambiri moti mu madera ena wakhala akugulidwa moposera MK3500.

Atalengeza za kukwera kwa Shugayu, a Salima ati aonjezeranso anthu oti azigulitsa shuga wawo kuti tsopano azipezeka ochuluka pa msika.

Kukwera mitengo kwa shuga kwadza pamene dziko lino likulimbana ndi kukwera mitengo kwa zinthu zochuluka.

Advertisement