Akweza madzi ku Blantyre

Advertisement
water tap

Ngati simufa ndi njala, ndiye mwina ludzu kapena kolera zitha kukuphani. A bungwe la Blantyre Water Board alengeza kuti madzi awo akwera mtengo.

Mu chikalata chimene bungweli latulutsa, a boma tsopano awapatsa chilolezo choti madzi akwere. Iwo ati madziwa akwera kuyambira pa 1 April, kutanthauza kuti pamapeto pa Mwezi uno ma bilu amene abwere akhala otutumutsa anthu.

Mwachitsanzo, bungweli lati tsopano azigulitsa madzi pa mtengo wa pakati pa MK1. 59 ndi MK2.22 motengera momwe anthu agwilitsira ntchito madzi.

Malinga ndi mulingo wa mmene a Malawi amagwiritsira ntchito madzi, pa tsiku munthu mmodzi okhala kumudzi amagwiritsa ma lita 36 amene potengela mtengo wa tsopano azikwana pafupifupi MK70. Pakutha masiku 30 ndiye kuti munthu otere azifunika ndalama zoposera MK2000.

Potengera kuti anthu okhala mtauni amagwiritsa ntchito madzi ochuluka, ndiye kuti pamwezi munthu mmodzi atha kufunika madzi oposa MK4000. Pa khomo la anthu asanu, ndiye kuti bilu ya madzi izipezeka yafika ndi kudutsa MK20, 000.

Madzi akwezedwa pamene a Malawi ochuluka akufinyika ndi kukwera mitengo ya zinthu, kusowa kwa ntchito ndi kusokonekera kwa za chuma.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.