Nkhondo yosumilana yavuta: naye Mneneri Chisa Mbele wapanikizana ndi Kampanikiza

Advertisement
Joshua Chisa Mbele

Komatu kulibe kupuma ku ma bwalo. Ili mkamwakamwa ya Dorothy Shonga osumira Mayi Easter Gondwe, a Joshua Chisa Mbele nawo awopseza kuti akamang’ala ku bwalo kuti a Gerald Kampanikiza akuwayipitsira mbiri.

Malingana ndi zimene alemba pa tsamba lawo a Chisa Mbele, ati ngati sachotsa mauthenga owazembelera kuti iwo ndi kathyali.

Mu sabatayi, kunamveka kuti bambo Chisa Mbele anagulitsa Mayi wina okhala dziko la Amereka malo oti ndi a boma. Ati malowa adawagulitsa pa mtengo wa 40 miliyoni Kwacha ya dziko lino.

Malinga ndi malipotiwa, zitadziwika kuti malowa ndi a boma, ati mayiyu yemwe dzina lake ndi Regina Mbowera adawauza a Mbele kuti abwenze ndalama zake. Iwo adamulembera cheke cha 40 miliyoni chomwe a bank adakachibwenza ati kunena kuti a Mbele alibe ndalama zotero ku akaunti yawo.

Malipotiwa atayamba kumveka, a Kampanikiza adali mmodzi mwa anthu amene adayamba kulemba za nkhaniyi. Mwa zina, iwo amatchula mozembetsa kuti a Chisa Mbele omwe amadzitcha okha kuti mneneri ndi kathyali ndipo adaba ndalama za mayiyo.

Koma lero pachiweru, a Chisa Mbele abwela pa tsamba la mchezo pomwe afotokoza mbali yawo ya nkhaniyi. Mukufotokoza kwawo ati panachitika kusamvana chabe ndipo sikuti iwo Ababa ndalama.

A Mbele apitiriza kuulula kuti kamba ka kuyipitsidwa kwa mbiri yawo, alamula maloya awo kuti asumire Mayi Mbowera. Iwo ati akufuna alipidwe ndalama zokwana 160 miliyoni za chipepeso.

A Mbele aopsezanso kuti atha kusumira a Kampanikiza ati chifukwa anadedeluka ndi nkhaniyi. Iwo ati samafuna kusumira a Kampanikiza chifukwa akuona kuti ndi mphawi chabe osowa chochita koma ati dzuwa likalowa a Kampanikiza asanachotse zimene analemba zokhudza iwo ndiye kuti awaswa ndi samani za ku bwalo.

Padakali pano zikuoneka kuti a Kampanikiza sakugwedezeka ndi nkhani zoopseza zomwe a Mbele anena.

Advertisement