Chiwerengero cha odwala Rubella chakwera ku Neno

Advertisement
Rubella Measles outbreak hits Neno District

Nthambi ya zaumoyo ku khonsolo ya boma la Neno yati pofika Lolemba pa 25 March, 2024, chiwerengero cha anthu omwe apezeka ndi nthenda ya Rubella chakwera ndipo chafika pa anthu 23.

Lolemba pa 25 March, 2024 thambi ya zaumoyo m’bomali yatulutsa chikalata chopeleka tsatanetsatane wa mmene zinthu zilili m’bomali potsati kubuka kwa matenda a Rubella sabata yatha.

Malingana ndi chikalatachi, anthu ena khumi ndi atatu (13) a tsopano, apezekaso ndi nthenda ya Rubella zomwe zapangitsa kuti chiwerengero cha anthu onse omwe apezeka ndi nthendayi chiyambileni chifike pa anthu makumi awiri ndi mphambu zitatu (23).

Chiwerengerochi chakwera kamba koti sabata yatha, anthu okwana khumi okha ndi omwe anapezeka ndi nthendayi ndipo poyambapo onsewa anali ochoka mudzi umodzi wa Manyenje pomwe pano zadziwika kuti nthendayi yafalikiraso m’midzi ina.

Chikalatachi chikusonyeza kuti kupatula mudzi wa Manyenje, nthenda ya Rubella yafikaso m’madera ena kuphatikiza Zalewa, Gobede, Sera, Donda komaso mudzi wa Mpakati m’boma lomweli.

Mwa midzi yonseyi, mudzi wa Manyenje ndi omwe uli pamwamba pa midzi yonse kamba koti ndi komwe kuli chiwerengero chokwera pomwe zadziwika kuti anthu khumi ndi anayi (14) apezeka ndi nthenda ya Rubella kuchoka pa anthu khumi sabata latha.

M’mudzi mwa a Gobede mwapezeka anthu asanu ndi m’modzi odwala nthenda ya Rubella pomwe m’midzi ya Mpakati, Sera komaso Donda kwapezeka munthu m’modzi-m’modzi odwala nthendayi.

Pakadali pano nthambi ya zaumoyo ku khonsolo ya boma la Neno yati ikupanga chothekera kuthetsa nthendayi ndipo mwa zina yawilikiza mauthenga odziwitsa anthu za kapewedwe ka nthendayi kudzera pa wayilesi komaso chinkuza mawu chomwe chikumazungilira m’madera akumeneko.

Malingana ndi unduna wa zaumoyo mdziko muno, wodwala nthenda ya Rubella, amaonetsa zizindikiro zofanana ndi yemwe akudwala nthenda ya Chikuku, koma chizindikiro chenicheni cha nthendayi ndi tinsungu tomwe timayambira kunkhope makamaka kuseri kwa makutu kenako nkumafalikira mkhosi ndi thupi Ionse.

Pakadali pano undunawu wati palibe mankhwala enieni ochiza nthenda ya Rubella ndipo nthendayi akuti imafala mwachangu kwambiri koma imatha yokha pakamatha sabata imodzi yokha.

Zina mwa njira zopewera nthenda ya Rubella ndi monga kukhara mwaukhondo zomwe ndikuphatikizapo kusamba m’manja ndi sopo, kutseka pakamwa potsokomola kapena kuyetsemula ndi kulandira katemera.

Advertisement