Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yati itseka miseu ina mzindawu

Advertisement
Newly constructed road in Blantyre

Pamene ntchito yokonza miseu ina ya mzinda wa Lilongwe idakapitilira, Khonsolo ya mzindawu yati ikhala ikutseka miseu ina monga wa CH 2+ 950 kukafika 2+980 (pafupi ndi Galaxy shop) kuyambila Lolemba pa 25 March, 2024 mpaka Lachisanu pa 6 April, 2024.

Malingana ndi chikalata chomwe wasainila ndi Bwanankubwa wa khonsoloyi, Dr McCloud Kam’manja, onse ochita malonda azitha kufikila mashopu awo podutsira ku Bread Talk komanso mseu oyang’anana ndi Lilongwe Musjid.

“Kuonjezera apo, ntchito zomwe tatchulazi zikachitika tidzatsekanso mseu wa CH 3 + 100 kukafika 3 + 120 pafupi ndi mzikiti wa Area 2”, yatero Khonsoloyi.

Chikalatachi chinaonjezera kunena kuti ntchito yomanga mseu watchuludwawu ikatha, Khosoloyi idzatseka mseu wa CH 3+100 kukafika 3+120 (pafupi ndi nzikiti wa Area 2) kuyambila Lolemba pa 8 April mpakana Lachisanu pa 19 April, ndipo ochita malonda azitha kufikila mashopu awo podutsila ku Bread Talk komanso Mseu wa CH 2+950 kukafika 2+950 (pafupi ndi Galaxy shop).

Advertisement