Anthu aku Chiputula ndi Ching’ambo ati akuvutika mayendedwe kamba ka kuduka kwa mlatho

Advertisement

Anthu okhala mma dera a Chiputula ndi Ching’ambo mu mzinda wa Mzuzu ali ndi nkhawa pa nkhani za mayendedwe kutsatira  kuduka kwa mlatho umene umalumikizitsa  ma derawa chifukwa cha mvura yamphamvu imene inagwa mu mzindawu.

Modzi mwa anthu okhudzidwa ndi vutoli amene amakhala dera la Ching’ambo, William Manda wati kuduka kwa mlathowu kwabweretsa vuto lalikuru kwa anthu amene amayendetsa ma galimoto komaso njinga za moto kudutsa pa malopa.

Koma khasala wa dera la Chiputula, Hewete Mkandawire wati pakadali pano khosolo ya mzuzu ilibe ndalama zoti ibwezeretse zinthu zimene zaonongeka mu mzindawu.

“Bajeti ya khonsoloyi inagawidwa kale ndipo ilibe ndalama zimene zingathandizire kubwezeretsa zinthu zimene zaonongeka mwadzidzi kamba ka kusintha kwa nyengo choncho ndikuyenera kugwiritsa ntchito ndalama zanga kuti ndibwezeretse mlatho  wadukawu.” a Mkandawire adatero.

Mmau ake mneneri wa khosolo ya Mzuzu, McDonald Gondwe wati khosoloyi ikudziwa bwino zinthu zonse zomwe zaonongeka kamba ka kuchuluka kwa mvura mu mzindawu.

Gondwe anati “Khonsolo yakhala ikupempha boma kuti lilowelerepo pa ntchito yobweretsa zinthu zimene zaonongeka maka misewu ndi milatho koma kufikira lero sitikulandira yankho lililonse.

Timadalira kwambiri thumba la Constituency Development Fund (CDF) komaso misonkno ina imene timatolera koma ndalamazi sizokwanira kuti zingagwire ntchito yobwerezeretsa zinthu zimene zaonongeka”. 

Mzinda wa Mzuzu wakhala ukulandira mvura masiku apitawa ndipo misewu ndi milatho yambiri yaonongeka chifukwa cha kuchuluka kwa madzi mitsinje yozungulira mzindawu.

Advertisement