Bushiri athandiza mwana odyetsedwa dowe wamuwisi

Advertisement

Mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG) Shepherd Bushiri wati ayamba kuthandiza mwana yemwe posachedwapa anaonesedwa m’masamba a nchezo akudyetsedwa dowe wa muwisi.

Posachedwapa, anthu ambiri m’masamba a nchezo anagwidwa ndi chisoni kamba ka kanema yemwe anthu anamugawana kwambiri yemwe amaonetsa mwana wina wa zaka khumi ndi ziwiri (12) akudyetsedwa mondokwa wa muwisi.

Malipoti akusonyeza kuti mwanayu anagwidwa akuba chimangachi m’munda wina chomwe amafuna akadye kamba koti kwawo kunalibe chakudya chili chose ndipo anthu atamugwira anamudyetsa chimanga cha chiwisicho ngati chilango kamba kopezeka akuba m’munda wa eni.

Potsatira nkhaniyi, lero Lachiwiri, mneneri Bushiri anatenga mwanayu pamodzi ndi mai ake kupita nawo ku sitolo ya PEP mu m’zinda wa Lilongwe komwe anampatsa mwai mwanayu kuti asankhe chovala chilichonse cha ku mtima kwake.

Bushiri wati wapanga izi kamba koti anali okhudzidwa komaso okhumudwa kwambiri ataona kanema yemwe amaonetsa mwanayu akudya chimanga chachiwisi mokakamizidwa ndipo walangiza anthu mdziko muno kuti adzikonda ana popeza ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.

“Ndipempho komaso langizo langa kupita kwa anthu onse mdziko muno kuti chonde tiyeni anawa tiziwakonda. Kaya si athu koma tiyeni tiwakonde kwambiri popeza ndi mphatso yomwe anatidalitsa nayo,” watelo mneneri Bushiri.

Kuwonjezera apo, mneneri Bushiri walonjeza kuti apeleka thandizo lili lonse lomwe lingafunike pa mwanayu zomwe ndi kuphatikizapo kumubwezeretsa ku sukulu yomwe akuti anasiya m’mbuyomu kamba kosowa chilimbikitso komaso thandizo.

Malipoti akusonyeza kuti mwanayu yemwe ndiochokera mmudzi mwa Mndola Mfumu yaikulu Kambwiri m’boma la Salima, anasiya sukulu ndipo m’malo kwake anayamba kugwira ntchito yaulonda yomwe pamwezi apamatsidwa K5,000 ngati malipiro yomwe akuti amathandizira mai ake.

Advertisement