Emmie Deebo wagulilidwa masamba pa fesibuku, pano ali ndiomutsata 1.7 miliyoni

Advertisement

M’nkuthwanima kwa diso, oyimba Emmie Deebo yemwe anali ndiomutsata ongokwana m’manjamu pa tsamba lake la fesibuku, tsopano wamusadabuza Patience Namadingo yemwe anali oyimba otsatidwa kwambiri kuno ku mpanje kamba koti pano msungwanayu akutsatidwa ndi anthu 1.7 miliyoni kutsatira kugulilidwa masamba ena a kunja a fesibuku.

Kampani yothandiza anthu a luso ya Akometsi yomweso imamuthandiza Emmie Deebo yemwe dzina lake leni leni ndi Emily Zintambila, ndi yomwe yatsimikiza za nkhaniyi Lamulungu pa 17 March, 2024 kudzera pa tsamba lawo la fesibuku.

Kampani ya Akometsi yati yamugulira Emmie Deebo masamba akunja angapo, kuwaphatikiza kenaka ndikulemba dzina la oyimbayu zomwe zapangitsa kuti oyimbayu pano akhala pamwamba pa oyimba onse m’dziko muno omwe ali ndi owatsatira ochuluka kamba koti tsamba lakeli pano lili ndi anthu olitsatira 1.7 miliyoni.

Kampaniyi yati ganizo lomugulira Deebo masamba ena akunja pa fesibuku ladza kamba koti oyimbayu amalephera akupeza mwayi oyimba ndi oyimba akuluakulu akunja omwe akuti ambiri mwa iwo amafuna kuyimba ndi munthu yemwe amatsatidwa kwambiri pa masamba anchezo kuphatikizapo fesibuku.

“Akuti dzulo dzulo lomweli anali ndi 120k followers koma lero wadzuka ali ndi 1.7 million followers, zakhala bwanji Akometsi kuti Emmie Deebo apezeke ndi 1.7 million followers? Nkhani yake ndi ya simple; Emmie wayimba ma collabo angapo akunja, koma kuti ma collabo amenewo atheke, ma artist akunjawo ambiri requirement yawo imakhala kuti Emmie Deebo akhale ndi either 1 million+ streams/views or 1 million+ followers pa imodzi mwa social media platform yake.

“Izi zinapangitsa kuti tipange invest ndalama zankhani nkhani pa platform yake kuti tifike 1 million+ followers. Tagula ma page amaiko angapo ndikuphatikiza kupanga page imodzi. Si mpikisano ndi oyimba ena, koma kudzikonzera njira ya international chifukwa ndikomwe maso athu aloza,” yatelo kampani ya Akometsi.

Akometsi yapitilira kufotokoza kuti tsamba loyamba la Deebo la fesibuku, linakalipo ndipo limenelo ndilomwenso azilidalira kuno ku kumudzi, pamene tsamba linalo lidzigwira ntchito oyimbayu akafuna kulumikizana ndi omutsatira am’mayiko ena, ndipo kampaniyi yanenetsa kuti zomwe yapangazi si mlandu.

Kampaniyi inaonjezera kuti m’mayiko akunja, anthu amalemekeza kwambiri oyimba yemwe akutsatidwa ndi anthu ochuluka m’masamba a nchezo, ndipo yati oyimba ambiri akuluakulu kuno ku Malawi amalephera kuimba ndi oyimba akunja chifukwa chosakhala ndi anthu owatsata ambiri pa masamba a nchezo.

“Artist akatchuka kwathu kuno, timadziwa ndife a Malawi kuti watchuka. Enawo alibe nazo ntchito ngati ma numbers sakuwoneka mochititsa chidwi. Tikunena pano, Emmie Deebo ali kunja ndipo lero (Lamulungu) akujambula video ya international collabo ndi crew yonena kuti pali madolo okha okha ndipo kukuchitika zakupsa.

“Koma zonsezi zatheka, komanso zambiri zitheka chifukwa choti anthuwo akuwona ma numbers amenewa. Tiyeni tikondwere kuti Malawi itha kutulutsa artist oti atha kutchuka nawo maiko ena akunja. To compete pa level yayikulu, we need to invest in our numbers,” yateloso kampani ya Akometsi.

Kampaniyi inamaliza ndi kumema a Malawi kuti amuthandizire oyimba Emmie Deebo ponena kuti oyimbayu ndi golide ndipo yati ikufuna chika chino chikamatha, maumboni koti oyimbayu ndikatakwe adzakhale ali mbwembwembwe.

Zisanachitike izi, oyimba Namadingo ndi yemwe anali ndi chiwerengero chochuluka cha anthu omutsatira, omwe ndi 1.2 miliyoni ndipo zatelemu zikutanthauza kuti Deebo ali pa mwamba ndipo Namadingo akubwera pa chiwiri ngakhale kuti iyeyu sanachite kugula masamba ena kuti afikile chiwerengerochi.

Advertisement