Gaba waitanidwaso ku Flames

Advertisement

Ngakhale kuti mphunzitsi wamkulu wa timu ya miyendo ya dziko lino a Patrick Mabedi sanatulutse mndandanda wa osewera akunja omwe wawaitana pa mpikisano wa mayiko anayi, zadziwika kuti Gabadinho Mhango yemwe anathawidwa ndi ndege chaka chatha, waitanidwaso.

Timu ya Moroka Swallows, ya ku South Africa, komwe Mhango ogoletsa zigoliyu amasewera ndi yomwe yatsimikiza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lake X pomwe yamuyamikira Mhango chifukwa cha kuitanidwaso kwake ku timu ya Flames.

“Tikufuna timuyamikire Gabadinho Mhango kamba koyitanidwa ka nambala 69 ku timu ya dziko la Malawi,” yatelo Moroka Swallows my uthenga omwe walembedwa mchingerezi.

Chaka chatha Gaba analephera kusewerela dziko lino m’mipikisano ingapo chaka chatha kuphatikiza masewero awiri odzigulira malo muchikho cha dziko lonse, FIFA pomwe anathawidwa ndi ndege mdziko la South Africa komwe akukhala pano.

Gaba atathawidwa ndi ndege yomwe imayenera kudzamusiya kuno kumodzi kuti anyamuke limodzi ndi osewera ena kupita ku Liberia, mphunzitsi wa timu ya Flames, Mabedi sanasangalatsidwe ndipo pomwe osewerayu anapempha kuti apatsidwe mayendedwe kuti akapeze timuyi mdziko la Liberia, Mabedi anakana kuti basi agwiritsa ntchito osewera omwe anali nawo.

Kupatula apo, katswiriyu sanasewere nawoso masewero amene Flames inasewera ndi ma timu ya Tunisia, mu ndime yomweyi ya chipulula mu mpikisano wa FIFA mwezi wa November chaka chatha chomwecho.

Kuitanidwa kwa Mhango pano, ndikamba koti Flames ikuyembekezeka kutenga nawo gawo m’masewero a mayiko anayi omwe ndi Zambia, Kenya ndi Zimbabwe, omwe achitikile mu mzinda wa Lilongwe kuyamba pa 21 mpaka 24 March chaka chino.

Advertisement