FAM ilowelelepo pa kusamvana kwa Mabedi ndi Gaba, watero Kanyenda

Advertisement
Gabandinho Mhango plays for Moroka Swallows in South Africa and Malawi national Football Team

As a way of supporting farmers, Bilal Trust- Central Region has distributed bags of fertilizer and seed packs to 1800 people in over 28 villages in Nkhotakota district.

Malingana ndi zomwe walemba Kanyenda pa tsamba lake la mchezo la Facebook, nkofunika kuti FAM iyitanitse osewerayu komanso mphunzitsiyu ndicholinga choti aunike mbali zonse ziwiri ndikuona kuti chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga ndi chani.

Kanyenda wapempha bungwe Loyang’anira maserewo a mpirawa  kuti ichite machawi pa  nkhaniyi.

Sabata latha, zidadziwika kuti Mabedi adasiya Gaba paulendo wa ku Liberia ponena kuti osewerayu alibe khalidwe pamene Gaba anati ndege idamuthawa. Osewerayu sadapatsidwe nawonso mwayi osewera masewero omwe adachitikira kuno ku mudzi ndi Tunisia.

A Kanyenda anapitiliza kunena kuti angakhale nkhaniyi ikunka nakulirabe, ndi zomvetsa chisoni kuti bungwe loyendetsa maseweroli silikuchitapo kanthu kuti chitsogolo chankhaniyi chidziwike.

Iye anafotokozanso kunena kuti iye ngati osewera wakale, alibepo mbali pa za nkhaniyi koma akupempha FAM kuti ichitepo chamuna pofuna kuthetsa kumsamvanaku.

Advertisement