Mapemphero anasokonekera ku Lunzu wansembe atathira bakera kwaya masitala

Advertisement
Malawi24.com

Zachitikanso lero mumpingo wakatolika ku Lunzu pamene wansembe wathira bakera kukamwa oyambitsa kwaya kamba koyambitsa nyimbo ya Aleluya mu nyengo ino ya lenti mpaka mapemphero kusokonekera.

Nkhani yonse ikuti a Edward omwe ndi oyambitsa kwaya amene amenyedwawa anayambitsa nyimbo panthawi yopereka mphatso ndipo nyimbo ili mkati panadzamveka mawu oti Aleluya.

Apa wansembeyo anadzambatuka ndikukathira bakera a Edward pakamwa kamba koti anayambitsa nyimbo ya Aleluya munyengo ya lenti.

Ndipo malipoti akuti wansembeyo atachita izi sanachedwe koma kulunjika nsana wanjira kwakwawo.

Apa mapemphero anathera panjira mpaka nkhosa sizinachitire mwina koma nazo zinabwelera panyumba.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement