Njonda ina yafa pomwe imafuna kuba Nsomba

Advertisement

Njonda ina yazaka 30 zakubadwa m’boma la Mangochi yatsikira kulichete itamira panthawi yomwe iyo imafuna kuba nsomba mumisampha ya asodzi amzake pa doko lina mnyanja ya Malombe.

Nkhani yonse ikuti mkuluyu yemwe dzina lake ndi Issaah Kamwendo, lolemba pa 26 February adazemba pakati pa usiku watsikulo ndikupita padokolo ndikuyamba kuba nsombazo mumatchera anzake.

Apa mwadzidzi eni matchelawo anatulukira pa malopo ndipo mkuluyo ataona kuti payipa anadumphira m’madzi ndikuyamba kuthawa.Iye atadumphira m’madzimo sadaonekenso ndipo izi zinachititsa jenkha anthuwo ndikuyamba kumufufuza mkuluyo koma sadampeze.

Dzulo lachiwiri pa 27 February ndipamene anapeza thupi lamalemuyu litayandama. Apa achipatala anapeza kuti malemuwa anafa kaamba kobanika.

Pakadali pano yemwe ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Amina Tepani Daudi watsimikiza zankhaniyi.

Malemu Kamwendo amachokera m’mudzi wa Namasiyano kwa mfumu yaikulu Chimwala m’boma lomweli la Mangochi.

Advertisement