Katswiri pa ulimi wati zoti dziko lino likolora chakudya chochuluka zikupereka mafunso

Advertisement

M’modzi mwa akatswiri pa nkhani za ulimi a Leonard Chimwanza, wati zotsatira zomwe unduna wa za ulimi watulutsa ponena kuti dziko lino likolola chakudya chochuluka ndizodzetsa mafunso kutengera ndi momwe mbewu ziliri m’minda yambiri mdziko muno.

Malingana ndi a Chimwanza, pakadali pano aliyense akutha kudzionera yekha momwe mbewu zaumira m’minda yochuluka kaamba kavuto lang’amba.

Iwo ati zoti dziko lino likolora chakudya chochuluka zikudzetsa mafunso kuti boma lakatenga kuti zotsatirazi ndi m’mene zinthu ziliri m’mindamu.

M’minda yambiri mbewu zauma.

Apa a Chimwanza ati zotsatirazi sizikugwirizana ndi momwe zimthu ziliri m’minda yambiri mdziko muno.Katswiriyu wapempha boma kuti lichitenso kafukufukuyu pofuna kupeza tchutchuchu wa momwe zinthu zilili m’minda yambiri mdziko lino.

Ng’amba yomwe yakhudza dziko la Malawi yaononga mbewu zochuluka m’minda yambiri pamene chimanga ndi mbewu zina zauma kamba kavuto lakusowa kwamvula.

Malingana ndi unduna wa za malimidwe, chimanga chokwana ma tani oposa 3.5 miliyoni chikololedwa kuno ku Malawi.

Advertisement