Pamene luso lojambula limayang’anilidwa pansi ndi anthu ambiri, nzika ya ku Malawi mu dziko la Zambia, Wonder Kumbikano yaponyera kwakuya luso lake lojambula kugwiritsa ntchito pensulo.
Nyamatayi yemwe zaka zake zakubadwa ndi makumi atatu ndi ziwiri wayipatsa moto pakuti akuphunzira kugwiritsa ntchito zipangizo zojambulira za makono monga blending stump, chacoal pencil, tombo mono zero eraser ndi manilla paper ndi zina.
Ena mwa akatswiri ophunzitsa zojambula odziwika bwino mu dziko la Zambia ngati Samson Sanda Chipeta ndi John Mwanza ndi amene ali patsogolo kumusula pakagwiritsidwe ntchito ka zida za makonozi.
“Luso lojambula kugwiritsa ntchito pensulo lili ndikuthekera kobweresa ndalama zakunja (Forex) ngati Boma kudzera kunthambi yazokopa alendo itayikirapo chidwi chachikulu ngati mmene limachitira dziko la Zambia,”iye anatero.
Wonder akuti akuyembekezereka kubwelera kumudzi kuno posachedwa chaka chomwe chino ndipo ndi okonzeka komanso ndi khumbo lake kuzagawana nzeru ndi ena aluso lojambula makamaka oyamba kumene.
Kupatula kujambula Wonder ndi namatetule pa nkhani yazamaphikidwe moti anakwanitsapo kuphikira wachiwiri wamtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulos Chilima komanso mtsogoleri opuma wa ku Nigeria a Olusegun.