Boma lawonjezera ndalama yopita kuthumba la CDF kufikapa 200 miliyoni

Advertisement
Malawi Members of Parliament

Kuwonjezera kwa ndalama zachitukuko za Constituency Development Fund (CDF) kuchoka pa 100 miliyoni kufika pa 200 million kwacha kunadzetsa chimwemwe chochuluka kwa aphungu ambili pamene nduna ya za chuma a Simplex Chithyola Banda anawuza nyumba ya malamulo zankhaniyi dzulo.

Aphungu ena ati kukweza kwa ndalamayi kuthandiza kuti aphungu akwanilitse kutumikira anthu m’madera awo pantchito zachitukuko zosiyanasiyana.

Ganizo lokweza ndalama zopita ku thumba la CDF ladza pamene phungu wina a Mike Ng’ombe Mwawa ndiwo adautsa nkhani yakufunikira kukweza ndalama yopita kuthumbali m’mwezi wa January chaka chino.

Mwawa adauzanso mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kufunikila komweza ndalamayi pa msonkhano wa chitukuko omwe udachitikila m’dela lake m’boma la Salima ponena kuti aphungu akadakonda ndalama ya chitukuko itakwezedwa.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement