M’mwambamu ndiye madzi alimo ndipo atsakamukamo ndithu — atero a zanyengo

Advertisement
Mvula Malawi

Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo m’dziko muno ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati kumwamba kudakali madzi amvula ochuluka kotero mvula yamabingu ikhala ikugwa m’madera ochuluka mdziko muno kufikira lachiwiri.

“Agulu mmwambamu ndiye madzi alimo ndipo atsakamukamo ndithu mokuti Lero ikuonekanso yamabingu, mawanso same same, Monday nso ndithu Lachiwiri nso, ndiye ngati sinakugwereni osada nkhawa ikufikani ndithu.”

Nthambiyi yanena izi lero pa tsamba lake la mchezo la Fesibuku pomwe imapereka tsatanetsatane wa momwe nyengo ikhalire lero loweruka pa 24 February 2024.

Pakadali pano madera ena kuphatikizapo mzinda wa Mzuzu ndi Lilongwe mvulayi yagwa kale.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement