Ndondomeko ya chuma cha dziko lino ikuyenera kuthana ndi vuto la njala, atero akatswiri

Advertisement

Katswiri pa kapezedwe ka chakudya dziko wati ndondomeko ya chuma ya chaka cha 2024/25 ikuyenela kuthandizira ulimi wa mthilila m’dziko muno pofuna kuthana ndi mavuto omwe adza kamba ka ng’amba yomwe yakhudza dziko lino.

Ronald Chilumpha, katswiri pa kapezekedwe ka chakudya chokwanila m’dziko muno, wati ndondomekoyi ikuyenela kukhala ndi mayankho okhazikika ku vuto la njala lomwe lili mdziko muno.

Katswiriyu wati paliso kufunika koonetsetsa kuti ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ikufikira alimi ambiri.

Poonjezera pa izi, Chilumpha wati nthawi yakwana yoti dziko lino liyambe kulimbikitsa ulimi wa mthilira pofuna kuthana ndi mavuto a nyengo ya ng’amba yomwe ikumachititsa alimi kusapeza mphindu mu ulimi wawo ngati momwe zilili pakadali pano.

Nduna yoona za chuma, Simplex Chithyola Banda, ikuyembekezeka kulengeza ndondomekoyi lero mnyumba ya malamulo.

Advertisement