Pomwe kudzigulira mavoti pa chisankho cha chaka cha mawa kuli mkati, m’mawa wa Lachinayi kunali “taonani taonani, zilikotu ziliko” mu mzinda wa Lilongwe pomwe aphungu awiri a chipani cha Malawi Congress (MCP) aliyese anagula bokosi la maliro a munthu m’modzi.
Nkhaniyi ikuti munthu wina yemwe ndiochokera kudera la kum’mwera cha kum’mawa kwa boma la Lilongwe watisiya mkati mwa sabatayi ndipo thupi lake limasungidwa ku nyumba ya chisoni pa chipatala cha Kamuzu Central munzindawu.
Malingana ndi malipoti omwe tapeza, chipwilikiti chinabuka m’mawa wa Lachinayi pa 22 February, 2024 pomwe malirowa amakatengedwa ku chipatalaku kamba koti zinapezeka kuti aphungu awiri a chipani cha MCP agula ma bokosi awiri a maliro amodziwa.
Zikuveka kuti malirowa atachitika, a Steven Baba Malondera omwe ndi phungu wa derali (Lilongwe South-East) komwe malemuwo amachokera, anagula bokosi lomwe anakalipeleka kwa anamfedwa kuti ayike thupi la m’bale wawoyo ndipo pa mbuyo pake nawo a Willard Gwengwe omwe ndi phungu MCP ku Dedza nawoso anachita chimodzimodzi.
A Gwengwe nawo anagura bokosi la maliro omwewo ngakhale kuti anachita izi mochedwelako kuyerekeza ndi phungu nzawoyo ndipo pa mapeto pake anthu ena okwiya analibweza bokosili mochititsa manyazi.
Malingana ndi kanema wina yemwe anthu akugawana m’masamba a nchezo, poyamba bokosi lomwe anagula a Gwengwe linalandilidwa ndikukwezedwa mgalimoto lomwe linanyamula zovutazi ngakhale kuti thupi la malemuwo linali litayikidwa kale mu bokosi lomwe anagula a Malondera.
Pomwe galimoto yonyamula zovutazi imafuna idzinyamuka kuchoka pa chipatalachi, zinthu zinatembenuka pomwe achinyamata ena anayamba kuyankhula kuti sizoona kuti maliro amodzi pagulidwe ma bokosi awiri ndipo kenaka anatsitsa mgalimotomo bokosi lomwe anagula a Gwengwe ndikulitsitsa pansi.
Mukanemayu yemwe ife taona, a chinyamata okwiyawa anamuuza Gwengwe yemwe anali atayima cha potelopo, kuti atenge bokosi lomwe anagulalo ponena kuti iyeyu siphungu wa dela la Lilongwe South-East kotelo sikunali koyenera kuti athandize maliro a mudelari.
Malipoti akusonyeza kuti a Baba Malondera asanakhale phungu ku dera la Lilongwe South-East, a Gwengwe anakhala phungu ku delari kwa zaka zingapo ndipo zikuvekaso kuti pa chisankho chikubwelachi, iwo adzapikisana nawo ku delari osatiso ku Dedza komwe ali pano.