Wapulumuka pamene khoti lati msungwana amati anagona nayeyo simwana

Advertisement
court

Njonda ina yazaka 30 zakubadwa, yapulumukira mkamwa mwa njovu pamene bwalo lamilandu ku Kasungu lamupeza osalakwa pa mlandu omwe amamuzenga ogonana ndi mtsikana yemwe amati ndi wa zaka 16.

Mkuluyu yemwe dzina lake ndi Lameck Banda, ananjatidwa  kamba koganizilidwa kuti anagonana ndi mtsikanayu ndi kumupatsa  pathupi kutsatira ndi momwe makolo amtsikanayu anakamang’alira kuti ndi wa zaka 16.

Nkhaniyi idalowa kubwalo la milandu komwe a Banda amayankha pa mlanduwu. Ndipo oweruza milandu Chakaka Nyirenda wapeza kuti msungwanayu ndi wa zaka 19 osati zaka 16 ngati momwe anakamang’alira makolo ake.

Apa oweluza mulanduwu anati  palibenso mulandu kamba kakuti msungwanayu simwana.

Banda adapalamula mulanduwu m’mwezi wa October chaka chatha ndipo makolo a msungwanayu anakamang’ala ku bwalo la milandu pa zankhaniyi.

Malingana ndi a Banda, iwo ati makolo a msungwanayu adachita izi pomwe iwo samkafuna kuti mwanayu akwatire ndi Banda.

Banda amachokela m’mudzi wa a Chitseka kwa mfumu yayikulu Njombwa m’bomali ndipo tsopano ndi mfulu kutsatira bwalo la milandu lati palibe mulandu.

Advertisement