Aphungu a DPP atulutsidwa mnyumba ya Malamulo

Advertisement

Aphungu oposa 20 a chipani cha DPP awatulutsa mu nyumba ya malamulo chifukwa anaima kuti alankhule pamene a sipikala anati manja awo ndi omangidwa pa za mtsogoleri wa otsutsa mnyumba ya malamulo ndipo akuona kuti a Kondwani Nankhumwa ndiwo adakali mtsogoleri otsutsa mnyumbayi.

Izi zinachitika pamene sipikala wa nyumbayi a Catherine Gotani Hara anawelenga zokambilana zomwe zinalipo lachitatu ndi komiti yowona za m’mene nyumbayi iyendere ikayamba kukumana ndipo anapempha mtsogoleri otsutsa kuti atsimikize kuti ndi zomwezo zomwe anakambilana.

Panachitika sewero pamene a Nankhumwa komanso omwe angosankhidwa kumene kukhala mtsogoleri otsutsa anaima pamodzi ngati atsogoleri otsutsa.

A Hara anati a Nankhumwa ndi omwe anali nawo pa zokambilana za patsikulo.

Aphungu oposa makumi awiri anaima mkumangoti akufuna alankhule ndipo izi zinapangitsa Sipikala wa nyumbayi kuwatulutsa.

Zokambilana mnyumbayi zinayimitsidwa kwa mphindi zokwana Khumi pamene Sipikala analamula aphunguwa kuti atuluke pogwiritsa ntchito ndondomeko ya nambala 105 koma anakana kutuluka.

Advertisement