Chipani cha DPP chati Mutharika ndiye yankho la a Malawi


Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chati Peter Mutharika ndiye yankho la a Malawi ndipo ngati mtsogoleri wachipanichi ndiwokonzeka kudzapikisana nawo pachisankho cha 2025.

Gavanala wachipani cha DPP mchigawo chakum’mawa a Imran Ntenje ndi womwe ayankhula izi pomwe chipanichi chidakonza misonkhano yoyimaima yomwe akuyitchula kuti Blue Convoy mu boma la Zomba.

A Ntenje adati malo onse omwe adayima kumayankhula, anthu adali kufuna kuti akumane ndi Professor Mutharika kuti amulongosolere zamavuto omwe akukumana nawo pamoyo wao watsiku ndi tsiku monga njala ndi kukwera kwa zinthu monga chimanga, feteleza ndi sopo.

Iwo adati chipani cha DPP chidakonza misonkhano yoyimaima kuti chikumane ndi anthu komanso chimve mavuto omwe akukumana nawo ndipo adati chipanichi chipitilirabe kuchititsa misonkhano yoyimaima kuti anthu adziwe kuti chidakali champhamvu.

A Ntenje adapempha anthu amene alibe chiphaso cha unzika kuti apite akalembetse kuti adzathe kudzaponya nawo voti pachisankho cha 2025.

‘Professor Peter Mutharika ali okonzeka kudzathetsa mavuto omwe anthu mdziko muno akukumana nawo monga kugona ndi njala, kukwera kwa zinthu zofunikira pamoyo watsiku ndi tsiku komanso ana aku univesite akulephera kupita ku school chifukwa chakukwera kwa fees,” Adatero a Ntenje.

Mu mau ake, mneneri wachipani cha DPP a Shadreck Namalomba adadandaula kuti pomwe chipani cha DPP chimachoka mu boma chaka cha 2020, zinthu monga chimanga, feteleza, sopo ndi zinthu zina zidali zotsika mtengo koma pano anthu akulephera kugula ndipo ali mu umphawi wadzawoneni chifukwa chosowa mtengo wogwira.

Iwo adati Boma la Dr Lazarus Chakwera lidanamiza a Malawi kuti likawasankha anthu adzidzadya katatu koma izi sizikutheka ndipo anthu akugona ndi njala m’malo mokudya katatu.

A Namalomba adati akafikitsa uthenga kwa Professor Peter omwe anthu apereka okuti adzawalamulire chaka cha 2025 ndipo akuti ali ndi chikhulupiliro kuti uthengawu akawuvomera.

Poyankhulapo, phungu wakunyumba yamalamulo mdera la Zomba Malosa Grace Kwelepeta adati mdera lake anthu akuvutika ndi njala komanso anthu mpaka pano akulephera kugula feteleza.

Phunguyu adadzudzula andale ena omwe akumasunga chimanga mnyumba mwao ndikumagayira anthu ochepa omwe akumasapota chipani chawo m’malo mogawira anthu onse mosatengera chipani.

Mdipiti woyimaimawu udayambira ku Gymkhana Club, mpaka ku Thondwe komwe adakayankhula ndi anthu a ku 6, miles, Mpunga, Chinamwali, Naisi, Domasi mpaka ku Namwera Turn Off

Ena mwa anthu odziwika bwino omwe adali nawo pamisonkhanoyo ndi monga Phungu wamdera lapakati mu mzinda wa Zomba Bester Awali, Phungu wamdera la Mulanje Bale Victor Musowa, Mkulu wa amai m’chigawo chakum’mawa Elube Kandewu, Dr Susuwere Banda yemwe ndi Phungu wamdera la Zomba Lisanjala, Chipiliro Mpinganjira ndi Yusuf Nthenda.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.