Mai wa zaka 78 waphedwa mu nyumba yake ku Chiradzulu

Advertisement

Apolisi m’boma la Chiradzulu akusakasaka anthu omwe apha  mai wa zaka 78 zakubadwa, Edina Makhumba.

Mbandazi zathawaso ndi foni ya manja tamabatani, Nkhuku folo, zofunda, ufa wachimanga olemera 5 kilogalamu komaso ndalama yokwana K20,000.

Mneneri wa apolisi ku Chiradzulu, Cosmas Kagulo,  wati izi zachitika m’mudzi wa Iidala m’bomalo.

Iwo anapitiliza kunena kuti mwana wa malemuwa  amene amakhala Ku Blantyre anayendera mai ake kumene anakapatsira matumba awiri a feteleza komaso ndalama yokwana K20,0000.

“Asadabwerere ku tawuni, mwanai anathandiza mai ake kuthira feteleza munda wawo wa chimanga.

“m’bandakucha wa tsiku la lero pa 9 February, 2023  mai wa anamuimbira foni mwana wawo koma ali nkati moyankhulana mbavazi zinafika ndipo kulumikiza kwawo kunasokonekera,” anatero a Kagulo.

Mwana wawo anaimbira achitetezo a mudzi kuti akafike kunyumbako kamba koti mayiwa amakhala malo awokhawokha.

Atafika kunyumbako anapeza chitseko chili chothyoledwa ndipo atalowa nyumba mo anapeza nthupi la a Makhumba lili pansi.

Anthuwa anatumiza uthenga Ku polisi ya Namadzi ndipo atafika apolisi pamalopa anapeza mayiwa atamangidwa ndi zigwe miyendo koma manja awo.

Thupili analitengera Ku chipatala cha Chiradzulu kumene achipatala apeza kuti mayiwa anamwalira kamba kovurazidwa mutu.

Mai Makhumba amachokera mudzi wa lidala mfumu yaikulu Mpama m’boma la Chiradzulo.

Advertisement