Katswiri pandale wati Chakwera asalonjezenso zochuluka

Advertisement
President of Malawi Lazarus Chakwera

Katswiri pa nkhani za ndale m’dziko muno a Lyford Chadza, walangiza Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ponena kuti uthenga wake wa SONA ukhale opereka chiyembekezo poona nyenyo zomwe dziko lino likudutsamo.

Katswiriyu wanena izi pamene mtsogoleri wa dziko linoyu lero akhala akutsekulira mkumano wa aphungu anyumba ya malamulo lero pa 9 February.

Malingana ndi Katswiriyu, mtsogoleriyu akuyenera kuwonetsetsa kuti zomwe alankhule zikhale zoti zingathe kukwanilitsidwa mu nthawi yochepa potengera ndi nthawi yomwe akhala nayo kuti tifike mchaka chamasankho.

Iye anafotokozanso kuti mtsogoleriyu sakuyenera kulonjeza a Malawi zochuluka kamba koti a Malawi akudikirabe ena mwa malonjezo omwe adachita mbuyomu.

Aphungu akhala akukambirana za ndondomeko ya zachuma ya chaka cha 2024 komanso 2025 ndipo nkumanowwu ukuyembekezereka kudzatha m’mwezi wa April.

Advertisement